Alipo anthu amene anawononga zinthu koma savomereza – Kunkuyu


Government through the Minister of Information and Digitalisation, Moses Kunkuyu, says Malawi Government has reached 798, 319 households with relief maize and will ensure all hunger-stricken households are reached with relief food.
Mkulu woona zokopa anthu mu chipani cha Malawi Congress Party (MCP), a Moses kunkuyu ati ndikofunika kuyamikila m’tsogoleri wakale, a Lazarus Chakwera Kamba koti amabwera poyera ndikuyankhula kuti pali magawo ena omwe sanayendetse bwino pamene anali m’boma.

Iwo ati alipo anthu ena amene anawononga zinthu koma samakhala ndi mtima ofuna kubwera pa maso pa a Malawi ndikuzafotokoza kuti pakuti sizinayende bwino.

Iwo anena izi potengera kuti m’tsogoleri wa chipani a Lazarus chakwera akhala akuyankhula m’mikumano ya chipanichi kuti anthu ena amati akawatuma amakapanga zinthu zina zosiyana ndizomwe atumidwa.

A Kunkuyu amayankhula izi pamene amacheza ndi tsamba lina lowulutsa mawu la LAB20 podcast mu pulogalamu ya the hot seat.

Iwo adati ndi zinthu zabwino popeza kuti a Chakwera amavomeleza zina mwa zinthu zomwe zinavuta, chifukwa nkutheka anthu pamene amakhala kumanena za nkhani yokhuza ulamuliro wawo pali zinthu zina zomwe sanawanenele bwino kapena kufotokoza zonse zonkhuza nkhaniyo.

“ngati akubwera kuti pakuti sitidatere, pakuti tidatere, tiyeni titenge chimenecho kuti pa mawa tizakumbukile kuti kunali President wa dziko, anali president wa Malawi Congress Party ndipo nthawi inayake adazichepetsa nkuzatiuza kuti pakuti sizinakhale bwino,” Adatero Kunkuyu

Kunkuyu anayankhulaso pa nkhani yokhudza kuyimitsidwa kwa nkumano wa a phungu a ku nyumba ya malamulo.

Iwo adati izi zitachitika anali okhumudwa kwambili chifukwa nkumano wa aphungu akunyumba ya Malamulo cholinga chake ndikukambirana za udindo umene aphunguwa alinawo potumikila anthu akudera komanso a Malawi.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading