Zadziwika kuti ana ena alephera kulandira katemela wa polio komanso chikuku m’boma la Kasungu kaamba ka zikhulupiliro za zipembezo komanso miyambo.
Izi zadwika pa mkumano omwe khonsolo yaboma la Kasungu ikupangitsa ndipo mwazina akukambirana za momwe ntchito za umoyo, maphunziro, chitukuko komanso zachuma zikuyendera m’bomali.
Komiti ya zaumoyo motsogozedwa ndi khansala Christopher Kamtambo ndiwo ananena izi pomwe amaapereka lipoti lokhudza momwe zaumoyo zikuyendera m’bomali.
Poyankhulapo pa nkhaniyi, mkulu owona za chisamaliro cha anthu m’bomali Ephraim Njikho ati kukaniza mwana kulandira katemela ndi kumuphwanyira ufulu kotero malamulo akuyenera kugwira ntchito yake.
Mkuluyu anati pakuyenera pakhale dongosolo labwino mwachangu lofikira ana onse omwe sanalandire katemela.
lipoti lomwe la za umoyo lomwe laperekedwa pa mkumanowu, lawonetsa kuti ntchito za umoyo zinakumana ndi mavuto akusowa kwa magulovesi ovala.
Pofuna kuthana ndi vutoli, adindo anagwiritsa ntchito ndalama zomwe akupeza kudzera kuchipatala cholipira cha Kasungu pogula magulovesiwa ndi mankhwala ena omwe anagwira ntchito m’zipatala zaulele m’bomali.
Pankhani yokhudza zamaphunziro akupulayimale, khonsolo ya Kasungu yayika ma zone okwana18 komanso sukulu zokwana 21 kuti ziyeselele P Class, yomwe ndi kalasi yomwe ana amaphunzira asanayambe Standard 1.

Pa mkumanowu zadziwikanso kuti kuchepa kwa nyumba za ogwira ntchito za aphunzitsi ndi adindo ena ndi vuto lalikulu mkulu owon zamaphunziro anati mkofunika kuti boma komanso madera atengepo gawo pofuna kuthana ndi vutoli.
Pakadali pano mkumanowu ukupitilira ndipo wachiwiri kwa wapampando wa khonsoloyi a Teresa Kanyukuta ndiwo akutsogolera zokambiranazi.
