Wogulitsa nyama ya galu wayithyola mukhothi


Nyama Yagalu- Malawi24

Njonda yomwe ikuyankha mlandu ogulitsa nyama ya galu ku Kasungu, inayithola m’maso muli gwa mukhothi pomwe inati inapha galuyo osati kuti igulitse.

Juma Sabiano wa zaka 49, wam’mudzi mwa Chisinga m’bomali, wamayankhula izi podzitetezera pa mlanduwu pamene amaonekera ka chiwiri ku bwalo la mirandu.

Sabiano ndi mzawo Chisomo Willard adanjatwa mwezi wa June m’mudzi mwa Chisinga powaganizira kuti amagulitsa nyama ya galu.

Ataonekera kubwali koyamba, iwo adaukana mlanduwu, zomwe zidapangitsa Chief Resident Magistrate Brian Sambo kuwuza mbali yaboma kubweretsa mboni pa nkhaniyi.

Juma Sabiano- Malawi24
Sabiano wati galuyu anali wandiwo pakhomo pake

Ataonekeranso kubwaloli a Sabiano anauza bwaloli kuti anapha galuyo ngati ndiwo yapakhomo osati yogulitsa.

Apa bwaloli layika tsiku la pa 12 August mwezi wamawa ngati tsiku lomwe lidzapereke chigamulo chake.

A Sabiano amachokera m’mudzi mwa Chiuta m’boma la Chiladzulu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading