NRB iyamba gawo lachinayi la kalembera wa ana


Nrb Registration- Malawi24

Bungwe la National Registration Bureau (NRB) lati liyamba gawo la chinayi la kalembera wa ana m’maboma anayi.

Malingana ndi kalata yachidziwitso yomwe wasayinira ndi mlembi wamkulu wa NRB, Patrick Machika, kalemberayu achitika m’maboma a Mulanje, Thyolo, Chikwawa ndi Nsanje.

Bungweli lati kalemberayu adzachitika kuyambira la Chiwiri pa 28 July mpaka la Chinayi pa 6 August 2026.

NRB yati cholinga chakalemberayu ndi kuonetsetsa kuti mwana aliyense walembetsedwa ndikupatsidwa chiphaso chomuzindikiritsa pa chingerezi birth certificate.

Bungweli latinso pomwe gawo lachinayi lakalemberayu likhale lili mkati, bungweli likhala likulembanso ana onse omwe akwanitsa zaka 16 ndi 17 zakubadwa kuti akhale ndi chiphaso cha unzika.

Apa bungweli lapempha ndikukumbutsa makolo kuti munthawi ya kalemberayu, ali ndi udindo olembetsa ana awo omwe sanakwanitse zaka 16 m’malo akalembera omwe akhazikitsidwa m’sukulu za pulayimale.

Bungweli latinso onse omwe akwanitsa zaka 16 ndi 17 akuyenera kupita ku ma Teacher Development Centre (TDC) omwe ali nawo pafupi kuti akalembetse chiphaso cha unzika.

“Olembetsa mwana (yemwe atha kukhala kholo kapena wachibale yemwe ali ndi chiphaso cha unzika) akuyenera kubwera ndi ziphaso za unzika kapena manambala a ziphaso za unzika za makolo enieni a mwanayo,” latero bungweli.

Ilo latinso kwa omwe akulembetsa chiphaso cha unzika akuyenera kutenga kholo lawo kapena anthu awiri omwe ali ndi ziphaso za unzika kuti adzawachitire umboni.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading