Wachiwiri kwa woyankhulira chipani chotsutsa boma cha Malawi Congress (MCP), Ken Msonda yemwe amadziwika bwino ndikusintha zipani, wati iwo ndi m’modzi mwa anthu omwe adathindizira kuyambitsa chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP).
Msonda wayankhula izi Lachisanu pa 12 June pomwe amacheza mu pologalamu ina pa wailesi ya kanema ya Luntha.
Mu pologalamuyi, Msonda wati m’mene malemu Bingu wa Mutharika ankayambitsa chipani cha DPP mu 2005 kuchoka ku UDF, iwo kuphatikizapo a Samson Msosa, Ken Zikhaleng’oma, Paul Maulidi ndi Sadik Bangazi, ndiomwe ankathamangathamanga kuti zonse zitheke mosavuta.
“Ife nde ma membala omwe tidayamba chipani cha DPP, onsewa mukuwaonawa ndi alendo,” watelo Msonda powonjezera kuti iwo sasinthha chipani pawokha koma kuti amachita kuyitanidwa chifukwa cha unamandwa wawo.
Mwachindunji, Msonda wati anayamba ndale 1992 koma anakhazikika kwambiri mu 1997 ndi chipani cha UDF, chomwe akuti adalowa Mulungu atawayankhula kuti atero.
Iwo adakhalaponso wachiwiri woyankhulira chipani cha Peoole’s (PP) pa nthawi yomwe a Joyce Banda anali mtsogoleri wa dziko lino.
Pakadali pano, potengera khalidwe losinthasintha zipani lomwe amadziwika nalo, anthu ambiri pa masamba a mchezo ati akuganiza kuti Msonda akuyankhula zonsezi kusakasaka polowela ku chipani cha DPP chomwe chikulamula pano.
“Uyu timumva kt wapita ku blue camp,” ndemanga ya Matias F. Phiri.
Sponsored
