Bullets yadya monona mwa Wanderers pomwe Silver Strikers yagonja koyamba lero


Mpokera, Phodo fire Bullets to derby glory as Wanderers’ short reign crashes in fiery showdown- Malawi24

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets tsopano yathetsa chilala chake chokanika kugonjetsa Mighty Wanderers kwa masewero anayi otsogozana pomwe lero yapambana 2-1, masewero a mu FDH premiership pa bwalo la Bingu National mu mzinda wa Lilongwe.

Bullets inachalira kuthetsa m’nyozo ndi chipongwe chomwe akhala akudutsamo pomwe Manoma akhala akuwagonjetsa m’maulendo anayi, iyoyo osachininkha chigoli.

Blessings Mpokera anagoletsera mu mphindi zoyambilira kudzera pa penote yomwe inadza otchinga kumbuyo a Wanderers, Stanley Sanudi, atagwetsa Ephraim Kondowe mu bokosi la ngozi.Wanderers inapanikizika kumayambiriro a masewerowa angakhale kuti inapeza mipata ingapo yomwe inamenyetsa zitsulo.

Chigawo choyamba chinatha mokomera timu ya Bullets.Chitayamba chigawo chachiwiri, Wanderers i inali pa mpira koma mipata yawo yambiri imamenyetsa zitsulo komanso otchinga pagolo pa Bullets, Innocent Nyasulu, anagwira ntchito yotamandika.

Pa mphindi ya chi 60, Maxwell Gasten anabwera ndi chipongwe china atalandira mpira ochokera kwa Yamikani Mologeni kuti masewerowo athere 2-0.

Pa mphindi ya 61 Manoma anadza ndi mkokomo ndipo anakwanitsa nawo kupeza penote yomwe Promise Kamwendo anagoletsa kupereka chimwemwe ndi chiyembekezo kwa Manoma.

Chifukwa cha kutentha kwa masewero a mu Blantyre Derby lero, oyimbira Mayamiko Kanjere anatulutsa m’bwalo Phodo wa Bullets ndi Gaddie Chirwa wa Wanderers kamba kochita khalidwe lomenyana lomwe ndi losaloledwa m’masewero a mpira.

Kanjere anaperekanso chikalata chofiyira kwa m’modzi mwa aphunzitsi a Bullets kamba kolalatira oyimbira ati posagwirizana ndi ziganizo zina zomwe anachita.

Bullets yatenga ma point onse atatu a m’masewero ake achitatu a mu FDH Premiership ndipo tsopano ili pamwamba pa m’ndandanda ndi ma point 7 pomwe Wanderers iri ndi ma point atatu mu masewero awiri.

M’masewero ena lero, Blue Eagles yawaza Silver Strikers 1-0 chigoli cha Benet Konyo, Red Lions yaphwanya Goshen City Dedza Dynamos 3-0 ndipo Kamuzu Barracks yagawana ma point ndi Karonga United zitathera 1-1 pa bwalo la Champions.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading