Sitinganeneretu ngati mabowo onse akhale atatsekedwa- Mwale


Sitinganeneretu ngati mabowo onse akhale atatsekedwa- Mwale- Malawi24

M’neneri mu unduna wazamasewero, MacMillan Mwale, wati pakadali pano sanganeneretu kuti pofika kumathero a sabatayi, adzakhala atatseka mabowo onse omwe anthu amalowera mwachinyengo ku bwalo la Bingu lomwe likuyembekezeka kuchititsa masewero atatu m’masiku otsatizana kumathero kwa sabatayi.

Bwalo la Bingu likuyembekezeka kuchititsa masewero a timu ya asungwana ya dziko lino Loweruka masana yomwe ikukumana ndi Nigeria.

Lamulungu padzakhala masewero a Mighty Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets, kenaka Lolemba, Masters FC ikhala ikukumana ndi LUANAR Mitundu, masewero amu FDH Premiership omwe adzachitike madzulo.

Titafika pa bwalori tinapeza kuti anthu ena anadula waya ozungulira bwalori mbali ya Area 47, momwe amagwiritsa ntchito kulowa osalipira.

Titafunsa a Mwale ngati pofika tsiku la masewerowa malowa akhale atakonzedwa, anati: “Sindinganeneretu chifukwa ndi malo oti akhala kanthawi ali ovuta, timati tikakonza anthu amaphwasulaso.”

Mwale anati ngati malowa sakhala atatsekedwa pofika masewero a FDH Premiership omwe ndiwolipira, ndiye kuti kudzagwiritsidwa ntchito njira zina monga kuchulutsa achitetezo mbaliyi kuti akamberemberewa asadzapeze mpata odutsa.

Titafunsaso ngati bwalori likhala lokonzeka kuchititsa masewero potengera kuti payipi zodutsa madzi a pansi pa bwaloli zimadalira magetsi omwe anadula kamba ka ngongole, a Mwale atsimikiza kuti zonse zikhala zili m’chimake.

“Tinakhalirana pansi mbali zonse zokhudzidwa pa nkhani yamagetsi ndipo zonse zikhala bwino. Komaso ndizoona kuti kuthirira bwaloli kumafuna magetsi koma pali njira ina yogwiritsa ntchito ma payipi opamtunda omwe akugwiritsidwa ntchito,” anatero Mwale.

Bwalo la Bingu ndilalikulu komanso lapamwamba m’dziko muno koma kwanthawi tsopano lakhala likuvutika ku nkhani ya magetsi, kutha kwa mipando yokhalira, kubowoledwa kwa mpanda otchinga bwalori komanso kubedwa kwa zipangizo zosiyanasiyana ku zimbudzi zapamalowa.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading