Nthawi ya a Chakwera inatha, 2030 simudzawaonanso – Major


Close-up of a serious Malawian politician in a blue suit.

M’modzi mwa anthu omwe akufuna kudzakhala mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress, Alex Major wati anthu asamayike dzina la m’tsogoleri yemwe alipo pakadali pano mchipanichi, Lazarus Chakwera ngati mmodzi mwa anthu odzapikisana nawo pa chisankho cha utsogoleri wa chipanichi (convention), patsogolo pa chisankho cha dziko lino chomwe chidzachitike 2030.

Poyankhula ndi LAB20 Podcast, Major wati malamulo a chipanichi sakulora a Chakwera kuti adzayimireso kamba koti nthawi yawo yokhala mtsogoleri inadutsa.

“Pakadali pano tilipo pafupifupi anthu asanu ndi mmodzi (6) omwe tawonetsa kale chidwi chodzapikisana koma musamaphatikize a Chakwera chifukwa anayimira kale kawiri ndiye malingana ndi malamulo, nthawi yawo inatha ndipo simudzawawonaso akupikisana nawo” anatero a Major.

Malingana ndi a Major, ati pakadali pano palibe munthu yemwe ali ndi ukadaulo wa mtsogoleri oposa wawo mu chipani cha MCP ndipo ati akulimba mtima kuti ndi omwe adzayimire MCP mu 2030.

A Major ati akadzakhala mtsogoleri wa dzino lino, adzawonetsetsa kuti athetsa katangale, agwiritsa ntchito zachilengedwe ndi ulimi zomwe dziko lilinazo pofuna kubwezeretsa mphamvu ya Kwacha, kupitiliza zitukuko zomwe ati zinabwera ndi MCP koma pano zinayimitsidwa komaso atchula kumbali ya ulimi kuti adzawonetsetsa kuti alimi akusangalala mdziko muno.

Mu 2014, Alex Major anapambana chisankho cha phungu wa nyumba yamalamulo ku dera lakumadzulo kwa boma la Kasungu.

Koma mkuluyu anagonja kwa khansala wake mu 2019, kenaka anapikisana nawo pa mpando wa mlembi wamkulu mchipanichi mu 2024 ndipo anagonjaso.

Patangotsa miyezi yochepa a Major anagonjaso chisankho cha chipulula ku dera latsopano la kumwera chakumadzulo kwa boma la Kasungu kenaka anagwa atayima pawokha pa chisankho cha a phungu pa 16 September 2025.Koma iwo ati kugonja konseku sikungawalepheretse kupambana ngati mtsogoleri wa MCP komaso wa dziko lino mu 2030.

“Kugonja konse kuja anthu ena ake ankachita kukonza powopa kuti ndidzatenga mtsogoleri wa chipanichi. Ndimaopedwa kwambiri ku MCP, ndimafusa zinthu zikamapanda kuyenda bwino ndie ena amanditenga ngati ovuta” anawonjezera motero Major.

Pakadali pano Major wati ali ndisapoti yochuluka kuchokera mmagawo onse a chipani cha Kongeresi zomwe zikumulimbitsa mtima ndipo wati sakutekeseka ndi anthu ena omwe akuchita pokhoso pamasamba a mchezo.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading