Njinga zikusokoneza zokopa alendo ku Sengabay


Bikes- Sengabay

Mfumu yayikulu Kalonga ya m’boma la Salima yati pali zinthu zingapo zomwe zikufunika kuwunikidwa kuphatikiza kuchuluka kwa njinga zakapalasa m’misewu zomwe zimasokoneza alendo omwe amapita kukasangalara m’bomali.

Mfumu Kalonga inayankhula izi poyankha zomwe ananena mkulu woyang’anira zokopa alendo m’boma la Salima, Wilfred Sagawa yemwe anauza Malawi24 kuti ntchito zokopa alendo m’bomali sizikupita patsogolo kamba koti anthu wamba sawonetsa chidwi chotenga nawo gawo.

Mwachitsanzo, Sagawa anati ngakhale ganizo lopanga bungwe loyang’anira zokopa alendo m’bomali, linachokera ku ofesi yawo kupita kwa anthu wamba mmalo moti anthuwa ndiwomwe amayenera kukhala patsogolo popanga bungweli.

“Mmadera mwawo muli nkhalamba zomwe zimakopa kale alendo, ngakhaleso zikhalidwe ndimagule amapanga ndithu koma sanadziwe ubwino omwe zokopa alendo ungawapatse kuzachuma” anatero Sagawa.

Koma Mfumu Kalonga titayankhula nayo, inati ntchitoyi siyamunthu mmodzi ndipo ikukhudza magawo ambiri oyenera kukonza kuti iyende bwino.

“Kupatula ofesi yazokopa alendo komaso anthu mmaderamu ntchito iyi imakhudza mbali zosiyanasiyana ngati apolisi, atolankhani, ku ofesi kwa DC ndimagawo ena” inatero mfumuyi.

Iwo ati mwachitsanzo misewu kuphatikizapo waku Sengabay komwe kuli zokopa alendo zambiri, umadzadza njinga zomwe zimasokoneza alendo yomwe ndi ntchito ya polisi kuti mseu udzikhala bwino.

Mfumuyi inatchulaso nkhalango ya Thunga ndi malo osungila zachilengedwe a Kuti ngati omweso ali okopa alendo m’bomali koma kulibe misewu yabwino zomwe ati ndi ntchito ya boma kuwonetsetsa kuti zonse zili mchimake.

Kotero mfumuyi inapempha magawo onse okhudzidwa kuti akhalire pamodzi ndikupeza njira zomwe zithandize ntchito zokopa alendo kuti ziyambe kuyenda bwino m’bomali.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading