Mu dziko lomwe anthu ambiri akudandaula za kuvuta kwa khobidi komaso ulova wonyanyira makamaka pakati pa achinyamata, ena akudzilemba okha ntchito ndi kumapha ma kwacha kuchokera muzoolerana; ulimi wa ntchentche, Black Soldier Fly (BSF pachingerezi. Ulimi wa ntchentche nchiyani kwenikweni? Uwu ndi ulimi omwe wafika m’dziko muno zaka pafupifupi zisanu zapitazi, ngakhale kuti ambiri sakuudziwa komaso ena akuwunyalanyaza dala. Ulimi wa ntchentche sufuna ndalama zochuluka kuuyamba; chofunika kwambiri ndi malo ochepa ochitira ulimiwu, zinyalala komaso ntchentchezo basi.
Poyamba, ntchentchezi zomwe sizibweretsa matenda ngati ntchentche zomwe ambiri tikuzidziwa, zimaikidwa malo okutiridwa bwino ndiukonde momwe pa kutha pa masiku ochepa zazikazi zimayamba kuyikira mazira.
Mazirawa kenaka amasanduka mphutsi, ndipo apa mpomwe nyasi zimafunikira.
Ntchentche ya BSF
Mphutsizi zimaikidwa mu makontena (onani chithunzi chachiwiri) momwe mumaikidwa zinyalala zomwe zitha kuolerana monga zotsalira za ku khitchini, nyasi za mmisika ndi zina. Mphutsizi zimadya nyasizi ndipo pakadutsa masiku a pakati pa 10 ndi 14, zimakhala zathera nsinkhu ndipo zimakololedwa.
Ntchentche m’khola mwake
Mphutsi zosakhwima zimatha kukhala chakudya chabwino cha nkhuku, pomwe ena zokhwimazo amaziumitsa nkupanga chakudya chaziweto monga nkhumba, nkhuku komaso nsomba.
Ngati mphutsizi sizingakololedwe zimabwerera nkukhalaso ntchentche zomwe anthu amathaso kugulitsana kuti akawete mwa njira yomweyi.

Mphutsi zikudya zinyalala
Kupatula kugulitsa ntchentche ndi mphutsizi, zotsalira za nyasi zomwe mphutsizi zimadya zija zimakozedwaso kukhala fetereza yemwe akatswiri akuti ndi wa bwino kwambiri.
Apa kuli ngati kupha mbalame zingapo ndi mwala umodzi; kupeza zakudya za ziweto, kupeza fetereza, kupha makwacha, ndi zina.
Malingana ndi Kettie Chisambi, Mkulu wa kampani ya North East Foods Limited, yemwe pano akuchita ulimiwu ku Nyambadwe munzinda wa Blantyre, zakudya za ziweto komaso feteleza zopangidwa kuchokera mu ulimiwu zimakhala zabwino kwambiri.
“Zakudyazi zimakhala zopereka thanzi kwambiri ku ziweto monga nkhuku, nsomba ndi nkhumba chifukwa mphutsizi zimakhala ndi michere yofunika kwambiri ku ziweto,” watelo Chisambi. “Feteleza wakeso ndi wa bwino kwambiri ku mbewu zathu.”
Chisambi wati pano kampani yawo idapatsidwa chilolezo ndi khonsolo ya mzinda wa Blantyre kuti itha kumayenda m’misika ndi malo osiyanasiyana munzindawu ndikumatolera nyasi zokagwiritsa ntchito pa ulimiwu.

Chisambi kufotokoza za ulimuwu
Kamba ka phindu ndi ubwino omwe wauona pa ulimiwu, Chisambi wati kutsogoloku akachitira ulimiwu ku Chileka komwe adagula malo okwana mahekitala 16, ndipo wati ngati bungwe la Malawi Bureau of Standards lingavomereze katundu wawo yemwe akuyesedwa, akuyembekeza kupita patsogolo kwambiri ndi ulimiwu pomwe wati kampani zikuluzikulu zingapo zaonetsa chidwi choti zitha kumawagula zakudya za ziwetozi komaso fetereza.
Pochitira umboni za ubwino wa ulimiwu, Folacy Mtonga, m’modzi mwa anthu omwe agwiritsa ntchito zakudya za ziweto kuchokera muulimiwu, wati nkhuku zomwe wakhala akuweta kwawo ku Edingeni ku Mzimba, zidasintha kwambiri pakutha pa masiku ochepa atayamba kuzipatsa chakudya chopangidwa kuchokera mu ulimi wa ntchentchewu.
“Ndinaona kukula bwino komanso thanzi pa nkhuku zanga nditayamba kuzidyetsa BSF feed,” watelo Mtonga.
“Chosangalatsa china nchoti zakudyazi nzotsika mtengo kuyerekeza ndi zakudya za nkhuku zopangidwa kuchokera ku nsomba zomwe timagula m’ma shop.”
Nawo a Lickson Alexander Magoboza, omwe ndi Technical Supervisor ku Triple F Farms munzinda wa Lilongwe, ati ataphunzitsidwa ndi Chisambi za ulimiwu, nawo adauyamba mosavuta ku farm yawo ndipo ati ndi ulimi owoneka onyozeka koma opindulitsa kwambiri.
“BSF feed ili ndi ubwino wambiri. Ili ndi ma protein ambiri, fats ndi calcium, imachepetsa zinyalala m’makomo ndi m’misika, komanso imapanga feteleza wachilengedwe yemwe alimi ambiri akusangalatsidwa naye.”

Mphutsi zokhwima
Magoboza watsindika kuti ulimi wa ntchentchewu ukuthandizira kuthetsa mavuto angapo nthawi imodzi, monga kupanga zakudya za ziweto zotsika mtengo, kusamala chilengedwe, komaso kupanga feteleza yemwe ali ndi kuthekera kobwezeretsa chonde mu nthaka.
Chinthu chimodzi chofunika kudziwa, ulimi siwokhudza ntchentche kapena mphutsi zokha, uwu ndi ulimi omwe ukulimbikitsa kusintha kaganizidwe ka anthu, poyamba kuona phindu pomwe pali zinthu zawonongeka.
Pakadali pano, mkulu wa North East Foods Limited, Chisambi, wamema achinyamata kuyamba ulimiwu, ndipo wati iye ali okonzeka kuthandiza onse omwe angafune kuyamba ulimiwu.
“Achinyamata yambani ulimiwu lero,” watelo Chisambi. “Ulimiwu sufunikira malo akulu kapena zinthu zokwera mtengo kuti muyambe.
Zipangizo zake n’zosavuta, zinyalala zimapezeka mosavuta, ndipo nthawi yopangira zinthu ndi yochepa. Mukhoza kuyamba pang’ono, ndikumakula kukhala chinthu chachikulu.”
Mosiyana ndi ma ulimi ena omwe amatenga nthawi yochuluka, amafuna kuleza mtima, ndalama zochuluka, komanso nyengo yabwino, ulimi wa ntchentche ukupereka zotsatira zabwino zochuluka mu nthawi yochepa komaso pa mtengo wotsika.








