Wachiwiri kwa mphunzitsi wa timu ya Mighty Wanderers, Macdonald “Nginde” Mtetemera wati chiyambireni kugwira ntchito ku timuyi palibe tsiku ngakhale limodzi lomwe timuyi idagwiritsapo ntchito juju pofuna kupamba masewero.
Poyankhula patsogolo pa masewero omwe Wanderers ikumane ndi FCB Nyasa Big Bullets loweruka pa bwalo la Bingu mu mpikisano wa NBS Charity Shield, Mtetemera wati m’mene ankalembedwa ntchito anauzidwa kuti zaka ziwiri zapitazo ena ku timuyi ankachita zazikhulupiro koma pano ndi mbiri yakale kutsatira lamulo la mtsogoleri wawo, Thom Mpinganjira.
Nginde wati ngati anthu anawonapo zofanana ndizikhulupiro zinali zongofuna kubalalitsa timu inayo chabe komanso osati zenizeni zothandizira timu kupambana.
“Ngati anthu anawona zinazake sikuti ndizenizeni koma kungofuna kubalalitsa adani mmaganizo,” anatero Mtetemera atafusidwa ngatidi akutsatira zomwe mtsogoleriyu ananena.
Pothirapo ndemanga za m’mene timu yake yakonzekera, Mtetemera wati achita chirichonse choyenera kuti timu yake ipambane.
Iye wati timuyi siikupita ndi lingaliro loti chaka chatha inagonjetsa Bullets katatu, ponena kuti mawa timuyi abwera mosiyana.
Mtetemera wati pakadali pano, osewera onse 28 omwe ali ku timuyi ali bwino ndipo palibe yemwe ali wovulala patsogolo pamasewerowa.
M’mau ake mtsogoleri wa osewera a Mighty Wanderers, Emmanuel Nyirenda wati akudziwa kufunika kwa masewerowa ndipo ndiwokonzeka kuchita bwino.
Aka kakhala kachinayi kuti ma team awiriwa akumane mu mpikisano wa chifundo ndipo masewero onse ambuyomu, team ya Bullets ndi yomwe yakhala ikupambana.
akanso kakhale koyamba pa zaka zitatu kuti ma team awiriwa akumanenso pa bwalori kamba kakuti adakumana komaliza m’chaka ka 2023 mu mpikisano wa FDH ndipo team ya Bullets ndi yomwe idapambana ndi zigoli zinayi kwachilowere.









