Tsogolo kuseri kwa Kadzamkodzo


Juliana Abudalla

Pambuyo pa vuto liri lonse, patsogolo pake pamakhala chisangalalo. Mmenemu ndimomweso ziriri pa amayi ena omwe adataya chikhulupiriro ndipo amasalidwa kamba kodwala nthenda ya Kadzamkodzo, “Fistula” pachingerezi, koma pano akusimba lokoma ataphunzitsidwa ntchito za manja.

Malingana ndi bungwe Malawi Liverpool Wellcome Trust, Kadzamkodzo ndi nthenda yomwe imaonjezera kukula kwa bowo lotulukira mkodzo maka kamba kamavuto ena pobereka, ndipo imapangitsa amayi kumangotaya mkodzo mosalekeza. Mwazina, kubereka wachichepere ndizina mwa zifukwa zomwe zimapangitsa vutoli.

Stafford
Martha Stafford

Amayi odwala nthendayi pena amasalidwa kamba koti amatha kumatulutsa fungo losakhala bwino. Izi zinali chimodzimodzi pa Martha Stafford wazaka 19, yemwe anachotsedwa chiberekero m’chaka cha 2025, atangobereka kumene mwana wake, zomwe zinabweretsa vuto la nthenda ya Kadzamkodzo.

“Atandipanga opareshoni bala linatukusira ndipo izi zinapangitsa kuti andichotse chiberekero koma mmalo mokhala bwino ndinayamba kumangotaya mkodzo zomwe zinapangitsa chipatala cha Kamuzu Central kuti chinditumize ku Bwaila” anatero Martha.

Atakhala kuchipatala cha Bwaila kwa mwezi umodzi, Martha anachira ku vuto lake la Kadzamkodzo ndipo anabwelera kwawo kwa Mpingo m’boma la Lilongwe komwe anakapitiriza kuthandiza mamuna wake kugwira maganyu wothandiza banja lawo.

Miyezi pafupifupi isanu atachoka pa chipatala cha Bwaila, Martha analandira lamya kumuuza kuti abwerere kuchipatalachi, osati kukalandira thandizo la mthupi mwake koma tsopano kukasulidwa pa ntchito yosoka.

“Ndinachitenga cha mtengo wapatali, ndipo sindinachedwe koma kuthamanga. Pano ndikukwanitsa kusoka ndipo ndikabwerera kwathu ndikaphunzitsa amunanga kuti mwina tikasiye ma ganyu ndipo apa miyoyo yathu ikasintha kamba ka luso ndi makina omwe tipatsidwe kuno,” adawonjezera Martha.

Msungwanayu sali yekha, Juliana Abudala, wazaka 39, wochokera ku Zomba, mfumu yayikuru Mulumbe, nayeso anachira ku nthendayi ndipo ali mu gulu la amayi 27 omwe akuphunzira nawo zosoka.

Abudala wati luso lomwe aphunzitsidwa, ndilapamwamba ndipo akabwerera kwawo akukasiya bizinesi yopanga zigege ndipo ali ndi masomphenya otsekula shop yazosoka.

“Pomwe ndinali mchipatala kamba ka vuto la Kadzamkodzo, mwana wanga anasiya sukulu kamba kosowa thandizo potengera kuti amunanga anatisiya koma apa ndili woyamika kamba kamaphunzirowa ndipo ndikukhulupira kuti ndikakayamba kusoka, mwana wanga akabwerera ku sukulu” anatero Abudalla.

Iye walimbikitsa amayi ena omwe ali ndivuto lochucha mkodzo kuti akuyenera kupeza thandizo kuchipatala cha Bwaila komwe moyo wa amayi sumamgosintha kuzofooka zamthupi zokha komaso kumakhala zinthu zosiyanasiyana zosintha tsogolo la amayi.

A Pauline Walles omwe akuphunzitsa amayiwa kusoka, ati ndiwokondwa ndimmene maphunzirowa akuyendera ndipo ati akukhulupira kuti akamaliza akakwanitsa kugwira ntchito ndikudziyimila pawokha.

Margaret Moyo, mkulu woyang’anira gawo la anthu odwala Kadzamkodzo pachipatala cha Bwaila wati ndikoyenera amayi ngati awa kupatsidwa maphunzirowa ponena kuti ambiri mwaiwo amasalidwa kumadera omwe amachokera.

Iwo athokoza bungwe la Lilongwe-Lingadzi Rotary Club kamba kathandizo lawo landalama zokwana 30,500 dollars za mdziko la America zomwe zagwiritsidwa ntchito pa maphunzirowa.

Chipatala cha Bwaila chinayamba kupereka thandizo kwa amayi odwala Kadzamkodzo mchaka cha 2010 ndipo pofika pano chikukwanitsa kuthandiza amayi pakati pa 350 kapena 400 pa chaka.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading