Sindikizani mapasipoti usana ndi usiku Mutharika walamula – Chisale


Sindikizani mapasipoti usana ndi usiku, Mutharika walamula - Chisale.

Mtsogoleri wa dziko lino Arthur Peter Mutharika walamula nthambi yowona zolowa ndi kutuluka mdziko (Immigration) kuti iyambe kupanga ziphaso zoyendera za omwe adalembetsa kuti akufuna ziphasoz usana ndi usiku.

Pokawona momwe ntchito yosindikiza ziphaso za pa ulendo ikuyendera mu mzinda wa Blantyre, wachiwiri kwa Nduna yowona za chitetezo cha mdziko a Norman Chisale ati mtsogoleri wa dziko lino walamula kuti ntchitoyi izigwirika ndi changu.

A Chisale ati mtsogoleri wa dziko lino walamulaso kuti akamabwelera kupita mu mzinda wa Lilongwe, theka la anthu onse omwe adalembetsa kuti akufuna ziphaso akhale atalandira ziphaso zawo.

A Chisale achenjezanso za mchitidwe wa katangale mu ma ofesi onse osindikizira ziphaso, ndipo wauza a Malawi kuti amene wapereka ndalama ya chinyengo akawatsine khutu kuti lamulo ligwire ntchito.

“Wina aliyense wa inu asayelekeze kupereka ndalama kwa munthu wina aliyense, yemwe wapereka ndalama kuyambira pa 1 April mwezi uno andipeze akangondilozera munthu amene wampatsa ndalamayo ndipo lamulo ligwira ntchito,” watelo Chisale .

Izi zikudza pomwe khamu la anthu silikukata m’ma ofesi a nthambi yopeleka ziphaso zoyendera, pomwe kuchedwaku nthawi zambiri kumakolezera mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu pakati pa ogwira ntchito ndi amkhalapakati komanso ofuna ziphaso.

Miyezi ingapo yapitayo a Chisale limodzi ndi adindo ena adapitanso ku ofesi ya nthambiyi mu mzinda wa Lilongwe komwe adatsimikizanso za kudana ndi mchitidwe wa katangale pa nkhani yofuna ziphaso zoyendera.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading