Ndikonza dziko lino, koma mundipatse ka nthawi pang’ono – Mutharika


Malawi24: Mutharika speaks during a rally despite the rain, showing resilience and leadership in Mal.

M’tsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika wabwereza kulonjeza kuti akonza mavuto osiyanasiyana omwe ali m’dziko muno, koma wapempha anthu kuti akhale odekha ponena kuti zambiri zidaonongeka ndipo kuzikonza afuna nthawi.

Mutharika walankhula izi madzulo a loweruka pomwe anaimitsidwa ndi khwimbi la anthu omwe anamuchingamira pomwe amafika munzinda wa Blantyre kuchokera ku nyumba yawo m’boma la Mangochi.

M’mawu ake, mtsogoleri wa dziko linoyu wati zinthu zayamba kale kuyenda bwino pomwe wati nkhani yodya chitedze kapena nyika ndi mbiri ya make dzana tsopano, ndipo wati zambiri zipitilira kukonzedwa.

“Palinso amene akudya chitedze kepena nyika? Tonse tikudya chimanga eti? Ine ndinanena kuti chimanga chitsika komaso mitengo ya zinthu zina ndi zina tiyesetsa kuti itsike kwambiri,” watelo Mutharika.

Komabe, iye wati anthu akhale odekha kamba koti zinthu zambiri zidaonongeka ndipo kuzikonza zifuna nthawi yochulukirapo.

“Koma mutipatse ka nthawi pang’ono chifukwa zinthu zambiri zinaonongeka kwambiri koma tikukoza ndithu pang’ono pang’ono, zinthu zosiyanasiyana zikupezeka, tikonza dziko lino.

“Koma kuti tikonze mupitilire kundipatsa ine support komaso chikhulupiriro, zina zimatenga nthawi koma mwaona nokha kuti zambiri tayamba kuchita,” adawonjezera Mutharika.

Mutharika adatchula sukulu zaulere ngati ena mwa malonjezo omwe boma lawo lakwaniritsa kale kufika pano, ndipo watsindika kuti akwaniritsaso lonjezo lopereka ngongole kwa achinyamata ndi amayi pofuna kuwapanga kukhala odzidalira pa chuma.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading