Suleman wamema anthu kuthandiza okhudzidwa ndi madzi osefukira


An image of Suleman Wamema wearing a judge's wig, speaking at a meeting about helping flood-affected.

Sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Sameer Sulemani, wapempha anthu onse akufuna kwabwino mdziko muno, kuti apereke chithandizo kwa maanja omwe akhudzidwa ndi mvula yamphamvu yomwe yakhala ikugwa m’madera ambiri a m’dziko muno.

Pempholi likudza pamene dziko lino lakhala likulandira mvula yowilikiza yomwe yadzetsa kusefukira kwa madzi ndikuwonongeka kwa katundu m’madera osiyanasiyana.

Sipikalayu wayankhula izi pa mkumano wakunyumba yamalamulo omwe uli mkati.

Naye phungu wa Rumphi West, Jona Adadawiza Mkandawire, wapempha boma kudzera mu Unduna wa Zantchito ndi Zomangamanga kuti uonjezere ndalama zokonzera misewu yomwe yawonongeka.

Mkandawire wati kuwonongeka kwa misewu kukusokoneza kwambiri mayendedwe ndipo kukhoza kuchedwetsa thandizo kufika kwa omwe akufunika.

Malinga ndi lipoti la bungwe loona za ngozi, DODMA, maanja okwana 9,598 akhudzidwa ndi mvula yamphamvuyi, pomwe 128 asamutsidwa m’madera awo.

Lipotili likusonyeza kuti anthu 13 ndi omwe atisiya, ndipo ena 35 avulala chifukwa cha ngozi zosiyanasiyana zokhudzana ndi kusefukira kwa madziku.

M’maboma ena monga Chikwawa, maanja oposa 1,500 akhudzidwa ndipo misewu ina yakhala yosadutsika, zomwe zikusokoneza ntchito zamayendedwe.

Lipotili latinso maanja pafupifupi 3,948 ndi omwe akhudzidwa mboma la Zomba.

Posachedwapa DODMA idalengeza kuti yayamba kale kugawa chithandizo kwa maanja omwe akhudzidwa, pamene maboma akupitiriza kuwunika kuwonongeka kuti adziwe momwe zinthu zilili.

Bungweli lapemphanso mabungwe othandiza, mabizinesi ndi anthu akufuna kwabwio kuti athandizire pa ntchito yopereka thandizo.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading