Pambuyo pa kuperekedwa kwa Bajeti ya 2026–2027 Lachisanu, chidwi cha anthu tsopano chikusunthira ku m’mene gawo la ulimi lidzapindulire ndi ndalama zokwana K931.1 biliyoni zomwe boma lapereka ku ulimi ku Malawi.
Ndalama zambiri zaperekedwa ku pulogalamu ya feteleza, kugula chimanga komanso ulimi wothirira madzi, zomwe boma likuyembekezera kuti zithandiza kuonetsetsa chitetezo cha chakudya ndi kuonjezera zokolola m’dziko muno.
Bajetiyi yaphatikizanso ndalama zogulira chimanga kudzera mu ADMARC, pofuna kuonetsetsa kuti dziko likhale ndi chakudya chokwanira komanso mitengo ikhale yokhazikika.
Kuphatikiza apo, boma layika ndalama zolimbikitsa ulimi waukulu kudzera mu ma mega farms omwe akuyendetsedwa ndi mabungwe a boma monga Malawi Prison Service, Malawi Defence Force komanso Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources, ndicholinga chofuna kuonjezera kupanga chakudya chambiri.
Pa mbali ya ulimi wamthilira , boma lapereka ndalama zokwana K241.1 biliyoni zotukulira ulimi wa midzi (rural irrigation development) kuphatikiza ndalama zothandizira ma scheme a anthu ammudzi. Izi zikuyembekezeka kuchepetsa kudalira mvula komanso kuthandiza alimi kukulitsa zokolola ngakhale nyengo isasinthe bwino.
12% ya bagetiyi ndiyomwe yaperekedwa ku ulimi, funso lomwe likutsalira ndi lakuti ngati ndalama zimenezi zidzafika pa nthawi yake komanso ngati nzika ndi alimi adzawona phindu lenileni m’nyengo ikubwerayi.