Kafukufuku wochitidwa ndi Platform for Investigative Journalism (PIJ) pa kasamalidwe ka National Economic Empowerment Fund (NEEF) ukuwonetsa kuti nkhaniyi si yokhudza kubweza ngongole zokha, koma ukuwulura m’chitidwe oyipa omwe ukuchitika kuti anthu asapindule pa ma pulogilamu oyenera kuwathandiza ndipo m’malo mwake, akumapindula ndi anthu okha okhawo andale.
NEEF inakhazikitsidwa kuti itsegule mwayi wa ndalama kwa mabizinesi ang’onoang’ono, achinyamata oyambitsa mabizinesi ndi amalonda a m’misika omwe nthawi zambiri amasiyidwa kunja ndi mabanki akuluakulu.
Komabe, kafukufukuyu akusonyeza kuti anthu ena omwe ali ndi ubwenzi wandale analandira ndalama zambiri kuchokera mu thumba limeneli, pomwe njira zokakamiza kubweza ngongole zinkakhala zofooka.
Izi zikuonetsa anthu odziwika pa ndale, kuphatikizapo omwe amatchedwa kukhala pafupi ndi Purezidenti wakale wopuma a Lazarus Chakwera, atsogoleri a nduna za boma, komanso mamembala a nyumba ya malamulo ochokera m’magulu osiyanasiyana a ndale, zomwe zikusonyeza kuti vutoli silingokhale la chipani chimodzi chokha. M’malo mwake, zikuwonetsa vuto lalikulu pa kasamalidwe ka ndalama za boma, pomwe njira zowunika ndi kuyankha zimalephera kulimbana ndi mphamvu za ndale.
M’mawu ake pa kuyankhulana ndi Malawi 24, katswiri wa ndale George Chaima anati izi zikuwonetsa mavuto aakulu pa kayendetsedwe ka boma pamene okhawo ali pafumi ndi a Boma amatha kupeza gawo lalikulu.
Komanso mapulogalamu othandiza anthuwa amakwanitsa kulemeletsa anthu omwe akulamulira chifukwa samaunikiridwa kwenikweni pa ndalama zomwe zikugwiritsidwa mu ntchito zoterezi.
Anawonjezera kuti kulephera kupeza kuyankha kwa anthu omwe ali ndi ubale wandale pa ndalama za boma kukupitiriza kufooketsa chidaliro cha anthu pa mapulogalamu a boma.
Iwo anati: “Simungapite kwa munthu wamphamvu kufuna kuti ayankhe pa ndalama zomwe anatenga kuboma. Nthawi zambiri mumakumana ndi chiphinjo, kapena milandu m’khoti yomwe imangoteteza munthu ameneyo.”
Ananenanso kuti mwadongosolo, pulogalamu iliyonse yomwe imakopa ndalama zambiri imatha kusokonezedwa ndi ndale.
Mzika zimalephera kufunsa chifukwa cha mantha kapena kuwopsezedwa, ndipo zimenezi zimapangitsa mapulogalamuwo kusowa njira zolimba zowunikira ndalama.
kafukufukuyu nagti uyu ndi wofunika osati pa pologalamu ngati a NEEF okha, koma pa zomwe boma la Malawi likuyendera ponseponse, makamaka mu nkhani za chitukuko cha anthu.
Kwa amalonda ang’onoang’ono ambiri amakumana ndi malamulo okhwima pa ngongole kapena kusiyidwa kunja, zimalimbikitsa maganizo oti kupeza chuma cha boma kumadalira kwambiri ubwenzi ndi mphamvu kuposa malamulo ndi mfundo.
Izi zikubweretsa funso lalikulu la kayendetsedwe ka boma: kodi ndalama zothandizira anthu ku Malawi zingathe kusanduka zida zothandizira andale ndi anzawo, osati zida zolimbikitsa kukula kwa chuma cha anthu onse?
Wolemba: Flora Jobe