Mundifufuze ndi mphuno momwe, sindinabe ngakhale 1 tambala – wakana Usi

Advertisement

Fisi anakana nsatsi! A Michael Usi omwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino muulamuliro wapitawu, ayima pachulu ndi kutchalenja kuti ngakhale atafufuzidwa ndi mphuno momwe, sangapezeke ndi mlandu wakuba ndalama za boma.

A Usi omwe amayankhula lachiwiri ku Dowa komwe amagawira anthu ovutika feteleza, amayankha pa lipoti lomwe linaperekedwa mnyumba ya malamulo yoti ofesi ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko muulamuliro wa a Lazarus Chakwera, idagwiritsa ntchito ndalama zoposa K15 biliyoni pa miyezi yochepa.

Koma a Usi ati iwo sakukhudzidwa ndikusakazidwa kwa ndalamaku ponena kuti iwo pomwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino samagwira ndalama.

“Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko samagwira ndalama, ma budget sizimamukhudza,” watelo Usi.

“Anthu akulankhulawo sakudziwa kuti ndili vice president nthawi zina mdipiti wa magalimoto anga mafuta ndimagula ndekha ndi ndalama zanga, ndimauzidwa kuti ndalama kulibe.”

Usi watiso ngati pali lipoti loti ofesi yawo idagwiritsa ntchito ndalama mosayenera, nkofunika kuti akuluakulu onse omwe amapanga za ndondomeko ya zachuma ku ofesi kwawoko ayitanidwe ndikuwafusa momwe ndalama zikunenedwazo zidagwilira ntchito.

Iwo ati anthu omwe akutchula dzina lawo pa kusakazidwa kwa ndalamazi akuchita izi chifukwa chongowada chabe ndipo anenetsa kuti iwo atuluka m’boma osabamo ndalama iliyose. “Omwe akunena zimenezi akungonenera kundida ineyo pa zifukwa zawo.

Koma nzotheka kulowa m’boma ndikutulukamo osaba, chitsanzo chake ndiine, ndinalowa kukhala nduna kenaka vice president, kulowa ndikutulukamo osaba or 1 tambala ndi chifukwa chake ndi kuti mutha kundifufuza ndi mphuno momwe simundipeza ndi mlandu wakuba,” wateloso Usi.

Iwo ati ndalama zomwe akugulira feteleza kumagawira anthu ovutika akumapatsidwa ndi abwenzi awo a m’dziko muno komaso ena ochokera mayiko akunja.

Advertisement