Nduna yoona Zachitukuko komanso maboma ang’onoang’ono, A Ben Phiri, yalengeza kuti boma lisunga ndalama za chitukuko cha m’madera zomwe zikuyembekezeka kukwera kuchokera pa K200 miliyoni kufika pa K5 biliyoni pa dera la phungu aliyense ndipo ziperekedwa mu ndondomeko ya za chuma ya chaka cha 2026 mpaka 2027.
Phiri anapereka chidziwitsochi pamene amakafotokoza dongosolo lalikulu la kusintha kwa kayendetsedwe ka maboma mu nyumba ya malamulo, lomwe laphatikizapo kuswa ma komiti onse a m’midzi ndi a madera (VDCs ndi ADCs).
Iwo ananena kuti mabungwe a m’maboma onse akhala akukhazikitsa ma komiti atsopano a zaka zisanu.Malinga ndi a Phiri, “Mabungwe onse a m’maboma ayamba kuchita misonkhano yoyamba pa Novembala 11, 2025, kuti asankhe atsogoleri atsopano komanso kuyamba kukonza njira zomwe zikugwirizana ndi ndondomeko ya chitukuko cha boma.”
Iwo anafotokoza kuti kusanthula kwa ndalamazi kudzayang’ana m’mene ndalama zimayendetsera komanso mmene zimawunikidwira, kuti zipindulitse anthu a m’mudzi.A Phiri adati:”
Ndalamazi zidzayang’aniridwa ndi ma Ma bwanankubwa a ma dera komanso akulu akulu ena, ndipo ntchito za CDF zigwirika kudzera mwa ma komiti atsopano a Village Development Committees ndi Area Development Committees.
Mipando ya ADC idzakhala ndi udindo wolemba ma fomu a ntchito motsogozana ndi mphungu wa nyumba zomwe zizikapelekedwa kwa Bwanankubwa wawo, ndipo izi sizikuphatikiza ma ward councillors.”
CDF ndi thumba la ndalama lomwe limathandiza ntchito za chitukuko m’ma constituency, ndipo kwazaka zapitazi lakhala chida chofunika kwambiri pothandiza kuimba paokha ndi chitukuko cha m’midzi. Komabe, lakhala likutsutsidwa chifukwa cha kusowa kwa kuwonekera bwino komanso kulowererapo kwa ndale.
Iwo ananenanso kuti aliyense amene adzapezeke akupeza kapena kugwiritsa ntchito molakwika ndalama za CDF adzayankhe molingana ndi malamulo.