Mukudikira sukulu za ulere? Muphonyana ndi mayeso aboma!

Advertisement

Pali chiopsezo choti ophunzira ena omwe ali ndi lingaliro lodyayamba sukulu zaulere zikayamba m’mwezi wa January chaka cha mawa ndipo adakali chikhalire, sadzakwanitsa kulemba nawo mayeso aboma amchaka cha 2026, ngati sakhala ndi mwayi olembetsa pomwe kalemberayu wayamba lero pa 10 Novembala ndipo udzatha pa 15 Disembala 2025.

Izi zikudza kutsatira pomwe bungwe loyang’anira mayeso m’dziko muno, la Malawi National Examinations Board (MANEB), lidalengeza sabata latha kuti kalembera wa ana a kalasi za mayeso m’masukulu a pulayimale ndi sekondale uyamba mwezi uno.

Malingana ndi bungweli, ophunzira a m’masukulu a boma ndi okhawo omwe salipira chilichonse pakalemberayu, kutsatira lamulo la boma loti masukulu akhale aulere.

Chiopsezochi chikubwera poti ophunzira ena omwe akufuna kudzalemba nawo mayesowa, akadali chikhalire ndipo akudikira kuti sukuluzo zitsegulire mumwezi wa January uku amza omwe ali ku sukulu akulembetsa mayina kuti adzalembae nawo mayeso amchaka cha 2026.

Izi zikutanthauza kuti akamadzayamba sukulu adzapeza kuti kalemberayu watha.

Poyankhulapo pa nkhaniyi, katswiri pa nkhani za maphunziro m’dziko muno, a Lexon Ndalama, ati ophunzira omwe akufuna kulemba nawo mayesowa akuyenera kuyamba kale sukulu ndi kulembetsa kuti asaphonye mwayiwo.

A Ndalama ati, ophunzirawa akuyenera asiyanitse zonena za anthu andale ndi zochitika zokhazika za boma ndi m’mene ntchito imayendera ndipo anthu andale ndi anthu andale ndithu ndipo amachita za ndale.

Iwo awonjezera kunena kuti ophunzira omwe ali ndi chidwi ayenera kupita kusukulu ndikupanga nawo ndondomeko yolembetsa mayina kuti adzakhale pa mndandanda wa omwe adzalembe nawo mayeso a chaka chamawa.

Pofuna kuti ophunzirawa ziwayendere, a Ndalama achenjeza ophunzira kuti ngati akufuna zasukulu, akuyenera kuti apange zasukulu kaamba koti akatengera za anthu andale ndekuti palibe chomwe apindule.

Advertisement