Dziko la Malawi lachita mwambo okumbukira asilikari omwe adamenya nkhondo


Dziko la Malawi lachita mwambo okumbukira asilikari omwe adamenya nkhondo- Malawi24

Dziko la Malawi lachita mwambo okumbukira asilikari omwe adamenya nkhondo zikulu zikulu za dziko lonse lapansi. Mwambo wachikumbutsowu wachitika m’mizinda ya Zomba, Lilongwe komanso Blantyre.

Ku Zomba mwambowu udachitikira pachipilara cha chikumbutso ku Cobbe Barracks ndipo Nduna yoona zakusasiyana pakati pa abambo ndi amayi a Mary Navicha ndi omwe adayimilira mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika.

Pamwambowo anthu adakakhala chete mphindi ziwiri kukumbukira mizimu ya asilikari omwe adamwalira pankhondozo.

Pamwambowo Nduna yoona zakusasiyana pakati pa abambo ndi amai Mary Navicha adayala nkhata yamaluwa motsatizana ndi Brigadier General Harrison Kalundula ndi Wachiwiri kwa Mkulu wa a Police Stain Bamusi Chaima komanso akulu akulu ena.

Mwambo onga ngati omwewu udachitikanso ku Lilongwe ndiku Mzuzu.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Jane Ansah ndiwomwe adayimilira m’tsogoleri wa dziko lino ku Lilongwe ndipo Wachiwiri kwa wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino a Enock Chihana ndiwomwe adayimilira m’tsogoleri wa dziko lino ku Mzuzu

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading