Anthu okhala ku Mvera m’boma la Dowa, omwe mabizinezi awo amadalira mafuta agalimoto adandaula kamba kavuto lakusowa kwa mafuta lomwe likukolezera kusokoneza ma bizinezi awo komaso ntchito zina ngakhale mafutawa adakwezedwa ndi bungwe la MERA.
Anthuwa amayankhula izi madzulo a Lachiwiri pa 4 November, 2025, pa malo omwetsera mafuta a Engen, ku Mvera pomwe tidayendera malowa.
Malawi24 inapeza kuti pamalowa panali mifolo italitali ya galimoto komanso njinga zamoto zomwe zinabwera kudzamwetsa mafuta koma mkuti munthawiyi, galimoto lodzatsitsa mafuta linali lisanatsitse.
Anthu ena pamalowa, anauza Malawi24 kuti tsopano kwatha pafupifupi sabata yatunthu malowa pakadalibe kanthu.
M’modzi mwa anthu omwe anati tisamutchule dzina, anati vutoli lasokoneza mabizinezi omwe amawadalira ndipo izi, zasokonezanso moyo wawo watsiku ndi tsiku wapakhomo.
Iwo apempha magawo onse okhudzidwa kuti awonetsetse kuti mafutawa azipezeka pafupifupi pofuna kuti omwe amadalira mafuta agalimoto pochita bizinezi zawo ukhaleko ofewa.
Nawo a Landirani Banda am’mudzi mwa Agogo, anati anabwera pa malowa kufuna kudzapeza nawo thandizoli angakhale kuti iwo anafika pamalopo pakanthawi ndithu koma amadikilirabe kamba koti mafutawo adali asadatsitsidwe.
Iwo anati, mafuta akumasowa kwambili, pamene mafutawo ndi okwera m’malo moti mafutawo azipezeka kamba koti adakwera mtengo, m’malo mwake akumakhalabe kuli zii osabwera zomwe zikuthandizira kusokoneza ma bizinezi.
Padakali pano, boma kudzera m’chikalata chomwe latulutsa, lati lithana ndi vuto lakusowa kwamafuta agalimoto lomwe lakuta dziko lino.
Malingana ndi chikalatachi, chomwe yasayinira ndi nduna yofalitsa nkhani, a Shadrick Namalomba, ati vutoli lakula kamba ka ziwawa zomwe zabuka mdziko la Tanzania.









