Alanda computer ya MEC kamba kofuna ndalama zake


Alanda computer ya MEC kamba kofuna ndalama zake- Malawi24

Mpungwe pungwe udabuka ku ofesi yowona za chisankho ya Malawi Electoral Commission (MEC) ku Zomba pomwe wapolisi wina adapita kukavutitsa pofuna ndalama zake zomwe adagwilira ntchito zoyang’anira chisankho pa 16 September ndipo adalanda computer ya bungweli ngati njira imodzi yofuna kukakamiza kuti amupatse ndalamazi.

Wapolisiyu yemwe dzina lake ndi Sub Inspector Ted Jumbe adapita kukafunsa ndalama zake zomwe adagwilira ntchito nthawi yachisankho ndipo adalanda makina a computer chifukwa chowawidwa mtima.

Zidatengera akulu akulu akhonsolo ya Boma la Zomba omwe adadziwitsa akulu akulu apolisi omwe adabwéra mwachangu kudzamutenga mzawoyo.

Bwana Mkubwa wa Boma la Zomba Reinghard Chavula watsimikidza zankhaniyi ndipo wati nkhaniyi ilimanja mwa Mkulu wa Polisi mchigawo chakum’mawa Commissioner Chikondi Mkwate Chingadza.

Koma ofalitsa nkhani za polisi m’chigawo chakum’mawa Superintendent Patrick Mussa wati timupatse kaye nthawi kuti ayambe wafufuza.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading