Ndili ndi chikhulupiro kuti tibweleranso m’boma – Chimwendo


Ndili ndi chikhulupiro kuti tibweleranso m'boma - Chimwendo- Malawi24

Mlembi wamkulu wachipani cha Malawi Congress Party (MCP), a Richard Chimwendo Banda ati ali ndichikhulupiro chonse kuti chipanichi chidzabweleraso m’boma.

Poyankhula ku nyumba yamalamulo pomwe amalumbira ngati phungu wanyumba yamalamulo ku dera lakummawa kwa boma la Dowa, a Chimwendo ati izi zidzatheka pokhapokha atawunikira ndikukonza zolakwikwa zawo.

“Chipani cha MCP chikanali champhamvu, munthu ukagonja umayenela kukhala pansi ndikudzifufuza kuti chalakwika ndichani. Ndili ndichikhulupiro chonse kuti tikakonza zolakwika zonse tidzabwelareso m’boma” anatero a Chimwendo Banda.

Iwo apemphanso otsatira chipani cha MCP kukhala wolimbika mtima komaso kuvomeleza kuti ndale umatha kugonja komaso kubweleraso.

“Takhalapo otsutsa, kenako olamura pano tabweleranso kotsutsa ndiye anthu akhaleso ndichiyembekezo kuti titha kubweleraso m’boma”

Iwo ayamikaso anthu aku mmawa kwa boma la Dowa powasankha kachitatu ngati phungu wawo.

Phunguyu wati anthu a dera lawo ayembekezere kuwatumikira ngati kale popezeka kumudzi ndi kutenga mavuta awo kukawapeleka ku nyumba yamalamulo.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading