M’phunzitsi wa timu ya Young Africans Sporting (Yanga) Patrick Mabedi wati osewera ambiri omwe akusewera mu timu ya Silver Strikers akuwadziwa bwino ndipo ena wawakuza yekha zinthu zomwe zithandizire kuti timu yake ipite mwa mtima onse awiriwa akamakumana loweluka mu mpikisano wa CAF champions league.
Mabedi amawuza atolankhani m’dziko la Tanzania kuti timu yake ya Yanga’ yakonzeka kupambana pa bwalo la Benjamin Mkapa mu mzinda wa Dar Es Salam’ m’dzikomo pomwe wati timu ya Silver ndi yofunika kukhala nayo maso chifukwa pamene ikubwera ikhala ndimtima ofuna kupambananso.
Iye wati osewera ambiri mu timu ya Silver anali nawo ku timu ya dziko la Malawi pomwe iye anali mphunzitsi ndipo ena wawakuza yekha koma izi sizifukwa zokwanila kupangitsa kuti Silver ayiyang’anile pansi.
Masewero achibwelezawa Silver Strikers ikupita kukakumana ndi Yanga’ koma ikutsogora kale 1-0 chigoli cha Uchizi Vunga mu masewelo oyamba omwe anali pa Bingu National mu mzinda wa Lilongwe.
Timu ya Silver ndi osewera ake 23, yanyamuka kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu International mu mzinda wa Lilongwe ndipo yafika mdziko la Tanzania kudzera pa bwalo la Julius Nyerere International mdziko la Tanzania.
Timu ya Young Africans, mkati mwa sabatayi yati anthu okawonelera masewelo akewa akalowa ulele, ndipo akatsiwri mdziko muno atin Silver isakayang’anile anthu posewera ndipo isakhale ndi mtima ofuna kufananitsa mphamvu koma ikhalabe chindunji chofuna kupambana.









