Tayimani kaye – waiyamba yokolopa APM pamene wapumitsa Kasakula, Suleman ndi Mdyetseni


MBC under scrutiny: The perils of partisan broadcasting- Malawi24

…tikuwafufuza koma zifukwa sitinena – boma
…katangale ndi chigololo ndizo zifukwa zake – ma ripoti

Akuluakulu atatu a kampani zomwe ndi za boma apemphedwa kuti abayima kaye ati ndi cholinga afufuzidwe. Izi ndi malinga ndi mlembi mu ofesi ya President ndi nduna zawo, a Justin Saidi.

Akuluakulu atatu amene ayimitsidwawa ndi wamkulu wa bungwe la nyumba ya boma loulutsa mawu la MBC, a George Kasakula. Iwowa aimitsidwa pamodzi ndi mkulu wa bungwe la MACRA, a Daud Suleman, komanso mkulu wa bungwe lobwereketsa ngongole la NEEF, a Humphrey Mdyetseni.

Malingana ndi malipoti, akuluakulu awa ati adziwitsidwa zoimitsidwa pa ntchito ngakhale kuti pano kampanizi zilibe nthumwi zoziyendetsa za Board kutsatira chiganizo cha a Mutharika chothetsa ma Board onse a kampani za boma mu dziko muno.

Atafunsidwa a Saidi kuti atchule zifukwa zomwe iwo ayimitsira anthuwa, iwo adangoti anthuwa akufufuzidwa. Iwo anati sanganene zambiri posafuna kusokoneza ntchito yofufuzayo.

Koma Malawi24 yamvetsedwa kuti anthuwa akufufuzidwa pa nkhani zosiyana-siyana kuphatikizapo katangale, kugwiritsa ntchito udindo molakwika komanso ati kukakamiza amayi ofuna thandizo kuti awagone.

“Mkulu wina pa oimitsidwawa amakhalira kuchita chipongwe azimayi kuti awapatse thandizo,” mkulu wina anatero potsina khutu Malawi24.

Iye anapitilizanso kunena kuti ena ayimitsidwa kamba koti amachita za katangale.

“Amapanga za u kamberembere mu ofesi, pena kulandira ziphuphu kumene,” anaonjezerapo.

Kalata zowaimitsa anthuwa pa ntchito zagawidwa pomwe sabata latha anthu ena omwe akuganiziridwa kuti ndi a chipani cha DPP anapita kukakwenya a Kasakula ku wailesi ya MBC ndi kuwalamula kuti apepese.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading