Kuvomeleza kwa Chakwera, manyazi kwa Mumba ndi Kabwira 

Advertisement
Mumba -

Pomwe m’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wavomereza kugonja pa masankho a chaka chino, manyazi a nkhaninkhani agwira a Vitumbiko Mumba, a Jessie Kabwira ndi Richard Chimwendo Banda omwe amakana zotsatira za masankhozi.

Kuvomereza kwa mtsogoleriyu kwayika gulu lamakanili kakashi kuti tsopano amalawi awawuzanji, pomwe adanamiza a Malawi kuti iwo ndi omwe apambana

Malinga ndi a Mumba komanso a Kabwira, chawo cha Malawi Congress (MCP) chidapambana masankho.

Ka guru kogalukira a Chakwera ka kadati a chipani cha Democratic Progressive (DPP) adachita kuchenjera posokoneza ma nambala a ma voti ena maka a ku madera komwe iwo amati mkuchipinda kwawo.

A Mumba omwe anayenda limodzi ndi a Chakwera kupita ku masankho a pa 16 September, anati iwo sakhala chete pomwe anawanamizira a Chakwera kuti ndi yemwe wawatuma kuti akane zotsatira.

M’tsogoleri wa dziko linoyu lero wati wavomeleza zotsatira za masankho pomwe wati zadziwikiratu kuti a Peter Mutharika ndi omwe apambana.

Lero nthawi ya 2 koloko wapampando wa bungwe loyendetsa chisankho la MEC Annabel Mtalimanja akuyembekekezeka kuti alengeze yemwe wapambana pa mpando wa mtsogoleri wa dziko.

Advertisement