Kanema wolawula uja adangondipaka – wakhetsa msonzi Rashley popempha kukhululukidwa
…wauza Driemo kuti asamuphe, asamumalize
Lero kwachera nkhani ya woyimba Rashley yemwe usiku wapitawu wakhetsa msonzi, kupempha chikhululukiro kwa a Malawi ponena kuti kanema wolawula wa mchaka cha 2021 uja adangopakidwa, ndipo wauza woyimba mzake Driemo kuti asamuphe.
Nkhaniyi yayambika pomwe Driemo amayankhula mu kanema ina m’dziko la Zambia momwe anati ku Malawi kuno kuli woyimba wina yemwe kuchokera 2021 akuvutika kamba koti a Malawi adamutuluka chifukwa chogulugusha.
Koma poyankha kudzera mu kanema ya pompo pompo yomwe adapanga pa tsamba lake la fesibuku usiku wa lachiwiri, Rashley yemwe dzina lake la pa msonkho ndi Happy Jumbe, wadzudzula “Kakaland Boy” ponena kuti wachitazo mchimodzimodzi kumupha.
“Zinthu zako ngati zikuyenda bwino ine ndine wokondwa. Ukapita ku mbali kayankhule zabwino koma usandiphe, usandipweteke, usandimalize. Tonse ndi a Malawi ngati ndinapanga zina zake sizinakusangalatse undikhululukire,” watelo Rashley.
Iye wauzaso Driemo kuti ngati woyimba, tsiku linaso atha kudzapanga chinthu cholakwika chomwe adzafuna a Malawi kuti amukhululukire, ndipo wanenetsa kuti si bwino kuseka mzake akagwa.
Pakanema yolaula yomwe adatchuka nayo mu 2021, Rashley wati adangopakidwa ponena kuti kanema weniweni ankamuonetsa iye ali ndi mkazi wake kuchipinda atavala zovala za mkati zokha, koma wati munthu wina waugogodi adayitenga nkuyiphatikiza ndi ina yolaula zenizeni.
Woyimbayu wapempha chikhululukira kwa a Malawi ndi kupempha kuti amupatseso mwayi wina.
“Kuti ndiyankhule izizi nchifukwa choti ndaona kuti zikundipha pang’onopang’ono. Ndikhululukireni, tipitilireso moyowu, ndisiyeni ndipitilize kukupatsani zimene ine ndili nazo a Malawi. Ndipatseniso mwayi wina. Ndikhululukireni, tisazakumbukirane nditamwalira,” wachondelera Rashley uku misonzi ikutsikira m’masaya mwake.
Pakadali pano Driemo sadayankhulepo za nkhaniyi.
One comment on “Kanema wolawula uja adangondipaka – wakhetsa msonzi Rashley popempha kukhululukidwa”
Comments are closed.










Nkhani izitha inuso, amalawi akhoza kukutulukani lero lomwe