Musawavotele! DPP ya Peter ndiyolephera, wasambwadza Kabambe


Kabambe

Mawere kuwilirana! Atasulidwa pa ndale ku chipani cha Democratic Progressive, Dalitso Kabambe yemwe akuyimira chipani cha United Transformation pachisankho chikubwerachi, wasambwadza m’tsogoleri wa chipani chake chakalecho, Peter Mutharika pomunena kuti ndiwolephera.

Kabambe amalankhura izi Lolemba pomwe anachititsa misonkhano yokopa anthu yoyimayima m’maboma a Chiradzulo komaso Mulanje.

Mwa zina, Kabambe yemwe adakhalapo gavanala wa Reserve Bank muulamuliro wa a Peter, wati DPP ya malemu Bingu wa Mutharika ndi yomwe inatumikira a Malawi bwino kuyerekeza ndi DPP ya a Peter yomwe awati kudali mavuto adzaoneni.

“Kodi pakati pa DPP ya a Mutharika ndi DPP ya a bingu, idagwira bwino ntchito ndi iti? Kutanthauza kuti DPP ya a Peter idalephera eti? Nde mukasankhabe DPP ya a Peter?” adafusa Kabambe.

Kuwonjezera apo, iye wati a Mutharika adalepheraso kutumikira bwino a Malawi pomwe adakhalapo nduna ya za maphunziro, nduna yowona za chilungamo komaso nduna yowona za ubale wa dziko lino ndi mayiko ena.

“A Peter Mutharika nawoso ali nduna ya maphunziro tinali ndi vuto losowa ufulu pa maphunziro. yunivesite ya Malawi adaitseka kwa nthawi yaitali,” adateloso Kabambe. “Ali nduna ya foreign affairs ndimomwe kazembe wa ku Britain adathamangitsidwa zomwe zidapangitsa kuti mayiko asiye kutithandiza ndi ndalama.”

Iye adawonjezera kuti ziganizo zina zomwe a Mutharika adapanga ali nduna, zidapangitsa kuti ndalama zakunja zisowe, zomwe zidachititsa mafuta agalimoto kusowa. Iwo atiso alinduna ya zachulungamo kunali kunyanyala ntchito ku mabwalo a milandu.

Apa Kabambe wamema a Malawi kuti asakavoteleso a Mutharika ponena kuti ndiolephera. “Chotelo tikavote mwanzeru, tisavotele anthu oti alephera.”

Koma polemba pa tsamba lake la fesibuku, mneneri wa chipani cha DPP, Shadric Namalomba wati Kabambe sakuyenera kuima pachulu kunyoza Mutharika lero, ponena kuti ndiwo adawasula komaso kuwasankha kukhala gavanala wa Reserve Bank. 

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading