A Malawi asambwadza kanema wa “wadya mtoliro,” Ati iwo atopa kudya “mtoliro”


WWadya mtoliroadya Ntoliro

A Malawi ambiri akuwonetsa kusakondwa kwawo ndi kanema yemwe akuzungulira m’masamba apa makina a intaneti yemwe akuwonetsa m’tsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera akunena kuti “game iyiyi ndukuwuzani ndi ya wadya mtoliro.”

Kanemayu yemwe wajambulidwa ku nyumba ya chifumu ya Kamuzu mu mnzinda wa Lilongwe wautsa mapirin pa chigwa pamene magulu osiyanasiyana akupereka ndemanga zawo pa kanemayu.

Anthu ena akuganiza kuti nyumba ya chifumu simayera kumangoikidwa pambalambanda mwa chisawawa ndipo ena akuganiza kuti kanemayu ndi onyazitsa potengera ndi mavuto omwe aMalawi akukumana nawo.

Ndipo anthu ena akuti kanemayu yemwe wasanduka nthabwala pa Tik Tok, Facebook komanso WhatsApp akuwonetsa ngati mtsogoleri-yu akungoseka mavuto omwe anthu akukumana nawo tsiku ndi tsiku monga njala, kusowa kwa ntchito ndi kugwa kwa ndalama ya kwacha.

Pothilira ndemanga pa tsamba la Facebook, Harry Phiri anati: “mtolirowo ife tatopa nawo ndipo muzidya nokha.Zimenezi tithana nazo pa 16 September mwezi wamawa chifukwa sitingasekelele masewera a mtoliro pamene ana athu akugona ndi njala.”

Ndipo a Mervis Chisawa analemba pa tsamba la X (Twitter) kuti: “Kuyitana aMalawi kuti adye mtoliro chifukwa cha mavuto omwe boma lanu lalephera kuthana nawo ndi chipongwe chachikulu.Dziko linotu lafika pomvetsa chisoni kwambiri.”

Titsindike kuti ndemanga kapena maganizo onse omwe alembedwa mu nkhaniyi si maganizo a Malawi24 koma maganizo a aMalawi.

Ngakhale palibe kutanthauzira kwenikweni kwa mawu omwe anayankhula a Chakwera, zikuonekabe kuti anthu ambiri sakuwona kanemayo ngati nthabwala koma chinthu chomvetsa chisoni komanso chonyoza.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading