Ilitu ndi funso lomwe a Malawi ambiri akufunsa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera m’masamba a mchezo osiyanasiyana pamene anena poyera kuti posachedwapa, boma lawo lilengeza mitengo yatsopano ya feteleza.
Poyankhula posachedwapa m’boma la Dowa pa misonkhano yawo yoyimayima, a Chakwera anati ali ndi chikhulupiliro kuti kutsitsa mtengo wa feteleza kungathandizile kuti alimi ambiri azitha kukwanitsa kugula feteleza-yu, ndikumakolora zochuluka.
Komabe, anthu ambiri awonetsa kunyinyilika ndi zomwe mtsogoleri-yu wayankhula ndipo ambiri akukhulupilira kuti iyi ndi nyambo yongofuna kukopera anthu kuti adzawavotele pa chisankho cha pa 16 September chaka chino.
Pothilirapo ndemanga pa nkhaniyi pa tsamba la nyumba yofalitsa nkhani ya Zodiak, Grace Make Theo adati: “Achikonza last year bolako.It’s already 2 letooo.”
A Wilson Memoir Mtegha nawo sadafune kuti angokhala chete pa nkhaniyi ndipo nawo analavula chakukhosi kwawo motele: “olo mutsitse kufika pa 1 pin, we will not vote for you.”
Ndipo a Amidu Komwa anawuza mtsogoleri wa dziko lino-yu kuti: “Uyimvera fungo ase voti.”
Titsindike kuti maganizo onse amene talemba mu nkhani ino si maganizo athu ife kuno ku Malawi24 koma ndi maganizo a aMalawi.
Komabe, paja amati chikumbutsa nkhwangwa mchisanu.Ife tikuwona ngati anthu ambiri ali okhumudwa potengera ndi zomwe amkalonjeza a Chakwera pokopa anthu mu chisankho cha mchaka cha 2020.
Iwotu adalonjeza kuti anthu m’dziko muno azizadya katatu ndipo kuti izi zitheke anati adzatsitsa mtengo wa feteleza kufika pa K4000 nkanthu.Pa nthawiyo, thumba la feteleza limagulitsidwa pa mtengo osapyola K22,000.Padakalipano, thumba la feteleza likugulitsidwa pa mtengo pafupifupi K200,000.
Komabe, zomwe adalonjeza a Chakwera asanasankhidwe zinali chabe maloto a Chumba chifukwa mtengo wa feteleza unayamba kukwera mosakhala bwino zomwe zinapangitsa kuti alimi ambiri, makamaka alimi ang’onoang’ono asamakwanitse kugula feteleza-yu.
Koma funso mkumati;Kodi aMalawi awakhulupiliranso a Chakwera akalengeza za mitengo yatsopano ya feteleza?









