Mafumu a mtundu wa achewa adzudzula mfumu Lukwa ati poyankhula mawu ogawanitsa mitundu


Senior Chief Lukwa

… katswiri pa ndale, Chaima ati mfumuyi idalakwitsa

Mafumu ena a mtundu wa a chewa adzudzula mfumu yaikulu Lukwa ya m’boma la Kasungu pobwera poyera ndikunena kuti anthu mchigawo cha pakati adzavotera chipani cha Malawi Congress (MCP) pa chisankho cha pa 16 September chaka chino.

Mfumu Lukwa idayankhula izi masiku apitawo pa mwambo wokweza mafumu 13 m’boma la Kasungu, pomwe inapempha mafumu onse a chichewa ndi anthu awo kuti adzavotele a Chakwera komanso aphungu ndi makhansala a MCP.

Lukwa adayankhulanso kuti mafumu a chewa m’chigawochi mothandizidwa ndi mfumu yaikulu ya Achewa m’maiko a Malawi, Mozambique komanso Zambia, Kalonga Gawa Undi ali pambuyo pa mtsogoleri wa chipani cha MCP a Lazarus Chakwera omwenso ndi mchewa.

Komabe, izi sizinakondweletse mafumu ena a chichewa m’dziko muno omwe atsutsana ndi ganizo la mfumuyi ponena kuti izi zikusemphana ndi mfundo za ulamuliro wa demokalase komanso ati zili ndi kuthekera kogawanitsa mitundu.

M’modzi mwa mafumuwa omwe sanafune kutchulidwa dzina anati: “Mafumu ndi oyang’anira chikhalidwe komanso mtendere, osati azipani.Zomwe anena a Lukwa zili ndi kuthekera kogawanitsa mitundu ya anthu komanso kubweretsa nkhondo.”

Ndipo pothilirapo ndemanga, katswiri pa nkhani za ndale, Dr. George Chaima, wati zomwe inayankhula mfumu Lukwa ndi zosayenera, ponena kuti mfumuyi singayankhulire anthu onse okhala mchigawo chapakati.

“Mavoti a mchigawo cha pakati sangaperekedwe ndi munthu m’modzi yekha monga a Lukwa.Ndi zolakwikanso kwambiri kuyankhula m’malo mwa anthu opitilira theka amene analembetsa mu kaundula wa mavoti mchigawo cha pakati,” anafotokoza Chaima.

A Chaima anafotokozanso kuti zomwe inayankhula mfumu yaikulu Lukwa ndi chizindikiro chongofuna kudzipezera cholowa kuchokera kwa a Chakwera.Iwo anapitiliza kunena kuti a Lukwa anayankhula mawuwa pongofuna kusangalatsa mtsogoleri-yu podziwa kuti andale ambiri amasangalala akamva zabodza.

Padakalipano, katswiriyu walangiza mfumuyi kuti iphunzire kukhala mtsogoleri olimbikitsa umodzi popeza m’dziko lino kuphatikizapo mchigawo cha pakati muli anthu a zipani zosiyanasiya.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading