Ati ngati mukunyoza a Chakwera mukufunika kumenyedwa, ndipo bambo Hetherwick Ntaba amene mmbuyomu anatchulidwapo kuti akudziwapo kanthu pa nkhani zokupha anthu a chi alubino azipereka kuti azithana ndi nonse onyoza a Chakwera.
Nkhalakale pa ndale a Hetherwick Ntaba wapempha mtsogoleri wa dziko lino kuti awalole iwo ndi anthu ena kutsina anthu onse onyoza a Chakwera. Poyankhula pa misonkhano yongoimaima yomwe akumachititsa a Chakwera mu chigawo chapakati, a Ntaba anadandaula kuti a Malawi ena akunyoza a Chakwera.
“Bwana, anthu akukuonani kufatsa bwana ndiye akumakunyozani bwana,” iwo anadandaula chotero. “Koma mukudziwa muli ndi achinyamata, ena ndi ife pano ometa pakati.”
Iwo anapitiriza kunena kuti a Chakwera awapatse chilolezo choti azipita kukamenya anthu onse onyozawa.
“Pano tikuti mutisiyire ife achinyamata anu kuti tikathane nawo anthu amenewa, tikawatsine,” anatero a Ntaba.
M’mene amayankhula izi ndiye kuti a Chakwera ndi mayi a kunyumba kwawo ali mu galimoto la mpandadenga akusekelera.
Mmbuyomu a Ntaba anatchulidwapo kuti akukhudzidwa ndi imfa za anthu a chi alubino mu dziko muno. Anthu ena adakhala akunena kuti mkuluyu ndi mmodzi mwa akuluakulu a ndale amene amasowetsa anthuwa kuti akawachitire zizimba.
