A Dalitso Kabambe ati anthu ogwira ntchito ndi ochita malonda satukuka msanga chifukwa ndalama zawo zimangothera ku boma kudzera ku misonkho mchifukwa chake ati akuyang’ana zodzatsitsa misonkho itatu.
A Kabambe ati akalowa m’boma adzatsitsa msonkho omwe amadulidwa anthu a pantchito wa Pay As You Earn (PAYE) kuchoka pa 30 pelesenti kufika pa 24.9 pelesenti komanso msonkho ogulira katundu wa Value Added Tax VAT kuchoka pa 16.5 pelesenti kufika pa 9.8 pelesenti.
Mtsogoleriyu watinso adzapungula msonkho wa ochita malonda kuchokan 35 pelesenti kufika pa 23.5 pelesenti la phindu lomwe amalonda apanga.
a Kabambe omwe akupikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko pa masankho a pa 16 September ati anthu a pantchito amaoneka ngati akulandira ndalama zambiri koma theka la ndalama yawo boma limatenga zomwe zimamuyika munthu kuti avutike kugula zinthu monga galimoto, kulipilira ana sukulu ngakhale kumanga nyumba kumene zomwe zimagwetsera ogwira ntchito ambiri ku ngongole za dziwongola dzanjanso dzokwera.
“Aliyense wapa ntchito amalipira 30% ku boma kudzera ku msonkho otchedwa PAYE, mogoyelekeza ngati amalandira 1 million kwacha ndekuti walipira 300 sauzande ku boma, iyeyo watsala ndi 700 sauzande kwacha koma sizinathere pompo, akapita kukagula zinthu, ndekuti 16.5% ikupitanso ku boma, ndekuti uyuyu achotsanso 115,500 kwacha kupitanso kuboma. Kuphatikiza zonse munthu m’modzi walipira 415, 500 kwacha kuboma mwachidule munthuyu sakulandiranso 1 million kwacha ayi koma 584,500 kwacha koma ku ntchito akuti walandira 1 million kwacha” anatelo a Kabambe.
M’mawu awo pomwe amachititsa misonkhano yawo yoyimayima mu mzinda wa Lilongwe, a Kabambe atsindika kuti misonkho ikulu ikuluyi ikupangitsa kuti dziko lisatukuke chifukwa chikoka chogula chimafooka.
A Kabambe atsindika kuti boma likukama Ng’ombe yowonda kale osayipumitsa pamene ena dziko lomweli sawudziwa msonkho.
Iwo ati kutsitsa misonkho kudzapangitsa mitengo ya zinthu itsike zomwe zidzakopenso ochita malonda maka akadzawona phindu lomwe akupezeka pa zotsatira za kutsitsa misonkho.
Apo mpomwe ati ochita malonda ambiri amathawa misonkho chifukwa cha kukula kwake, koma kutsitsa misonkho, ambiri adzakhala opanda zifukwa zozembera zomwe zidzadzetse ndalama zambirinso.
Mu mfundo zawo, a Kabambe ati adzayika ndalama zokwana 500 billion kwacha Ku ntchito zopanga katundu, 500 billion kwacha ku zokopa alendo, 500 billion kwacha Ku ntchito za migodi, 500 billion ku ntchito za ulimi ndi 100 billion kwacha ku ma khonsolo a pa boma pa chaka.









