“Mukandipha mundidya?” – Usi wati sakuopa kuphedwa


Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Michael Usi, akupitilirabe kulavula moto pomwe waulura kuti pali anthu ena omwe akupanga chiwembu chofuna kuthothola moyo wake, koma wati sakuopa.

Poyankhula Lachitatu ku Chigumula munzinda wa Blantyre pa misonkhano yake yoyimayima, Usi wati walandira kilipi (audio clip) momwe anthu ena amakambirana zoti achotse moyo wake.

“Wina wache wakomweko zampweteka kuti mukufuna kumupha Usi walakwa chiyani, nde wangoponya ka audio-ko,” watelo Usi powuza khwimbi lomwe linasonkhana.

Usi wati ndiodabwa kuti asilikali ake akumauzidwa ndi akuluakulu aboma kuti apeleke kaye mfuti zawo, zomwe wati zikumawapatsa maganizo pa zolinga za anthuwo.

“Tsopano akawalanda mfutizo akhalaso asilikali? Akufuna anditani? Akumanena kuti ameneyu timpweteke, ameneyu ku Lilongwe asabwere, ine nditha kuyenda wapansi kukafika konko. Ine ndingaope kufa? Ndikafa ndidziva kupweteka?” wateloso Usi.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu wati pasamakhale kuopsezana pomwe ena akufuna kukonza zinthu kuti dziko lino likhale lokomera aliyise.

Kuonjezera apo, Usi walembanso pa tsamba lake la fesibuku kuti walandidwa imodzi mwa galimoto za pa m’dipiti wake yomwe akuti yapelekedwa kwa m’modzi mwa akuluakulu a chipani cha MCP.

“Galimoto ya pa mdipiti wa vice president, Lead or Pilot Vehicle yomwe imanyamula achitetezo anga yalandidwa ndikuperekedwa kwa munthu oti si vice president. Galimoto yi ndi ya boma osati yachipani.

“Inetu olo atandiranda ma galimoto onse kuti ndiyende pa wheelbarrow sindingawone vuto chifukwa ndakula ndikuyendetsa chingelengele. Chomwe ndikudana nacho ine ndi katangale ndi umbava!” walemba choncho Usi.

Masiku amenewa, pakhala pali kusinthana mawu pakati pa Usi ndi akuluakulu aboma pomwe iwo akudzudzula kuti m’boma mwachuluka ukapsala.

Lachiwiri mneneri wa chipani cha MCP adauza a Usi kudzera pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe kuti ngati akuona zolakwika zambiri m’boma, angotula pansi udindo wawo.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading