Patangodutsa masiku ochepa chabe, wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino Michael Usi atadzudzula akulu akulu ena a boma amene akusakaza chuma cha dziko lino pa msonkhano wa ndale umene anachititsa mu mzinda wa Blantyre, lero galimoto imene imanyamula achitetezo yalandidwa.
Kudzera pa msonkhano ongoimaima m’mawawu umene anakonza, A usi ati iwo sakunjenjemera ngakhale atalanda galimoto zonse zimene anapasidwa ndi boma.
“Inetu olo atandiranda ma galimoto onse kuti ndiyende pa wheelbarrow sindingawone vuto chifukwa ndakula ndikuyendetsa chingelengele,” iwo anatero.
Wachiwiri kwa tsogoleriyu wakhala akudzudzula m’chitidwe wa katangale umene wa manga nthenje m’boma maka kwa akuluakulu amene akugwira ntctio ma unduna osiyasiyana a boma kudzera minsonkhano yokopa anthu.









