Cement ngambwingambwi akubwera, mitengo yake igwa pompano – walonjeza Mumba


Mumba Malawi

Inu amene mwakhala mukulira nkhani ya cement, dekhani mtima wanu pansi. Ena amene mwayamba kumanga nyumba zophoma ndi matope, nanunso konzekani kuti muyambiranso kumanga ndi simenti. A nduna a Vitumbiko Mumba ati athana ndi vuto lakusowa komanso kukwera mtengo kwa simenti ndipo akhala akupezeka paliponse mu dziko lino.

Nduna yoona za malonda amenenso atha kuzakhala wachiwiri kwa dziko lino ngati a Lazarus Chakwera angakwanitse kupambana pa chisankho cha pa 16 Sepitemba, a Vitumbiko Mumba lero auza mtundu wa a Malawi kuti iwo apeza njira zothanirana ndi kampani zopanga simenti zimene zikufuna kugwetsa boma.

“Kusowa kwa simenti uku, zikuchitika ndi ndale,” anatero a Mumba pa tsamba lawo la Facebook pamene amalengeza kuti iwo akwanitsa kuitanitsa matumba a simenti kuchoka mu dziko la Zambia.

“Kampani zopanga simenti zinatiuza kuti tiwapatse njira zofewa kuti azigulitsa simenti mu dziko muno, ife tinawapatsa, koma mmalo mwake simenti angokwerabe mtengo, kodi iwowa akufuna chani?” anadabwa chotelo a Mumba amene mmbuyomu anakwenyedwapo pakhosi ndi kusowa kwa shuga mpaka amathandizira nawo kulondera galimoto zonyamula shuga.

Iwo anati apita ku Lusaka mu dziko la Zambia kumene akakumana ndi nduna ya za malonda kumeneko ndipo agwirizana kuti tsopano dziko la Zambia lizitumiza simenti mu dziko la Malawi kuti ayambe kupezeka ndi kuthandiza kugwetsa mitengo yake.

“Ndikunena pano, tamvana kale za matumba 12 sauzande amene akubwera. Iwo azifika lachinayi kapena lachisanu lomweli,” iwo anatero.

Koma owakayikira osalephera, ena anati zimene akuchita a Mumba zili ngati zomwe akhala akuchita ojiyira a chipani chawo cha Kongeresi pomapita akulengeza kuti mafuta akubwera mu dziko muno pamene anthu ali pa mzere wamafuta.

“Mwayambapo, ngati a mafuta aja, tangopangani zoti simenti apezeke ndipo atsike mtengo,” wina analemba monyodola chotero pa Facebook pomwepo.

Matumba a simenti akhala akukwera modabwitsa pamene mu madera ena anafika pa 48 sauzande kuchoka pa 30 sauzande. Zonsezi zachitika mu sabata imodzi.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading