Pa misonkhano yomwe anakonza lero, m’tsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) Dalitso Kabambe wati poyang’ana momwe zinthu zakwelera mitengo komanso kusokonekera kuchokera mchaka cha 2020, kuvotelanso mtsogoleri yemwe alipo pano a Lazarus Chakwera ndekuti kukhala kuvulaza ndi kuwapha aMalawi motheratu tsopano.
A Kabambe ati a Chakwera pomwe amatenga boma zinthu zinali zomvelera koma pano mitengo yake ndi yosafikilika ndipo ati chiwopsezo cha kuwonongeka kwa zinthu kuposa pakali pano chilipo ngati aMalawi asankhe molakwika posankhanso a Chakwera.
Polankhula pa Matapila ku dera la Lilongwe Mpenu, a Kabambe ati mbewu ya Chimanga yolemela 10 kilogalamu inali pa 16,000 kwacha pamene pano ili pa 138,000 kwacha, ndinso feteleza anali pa 18,000 kwacha pano waposa 160,000 kwacha thumba la 50 kilogamu.
A Kabambe anatinso kuchoka kwa sopo pa 50 kwacha kufika pa 1, 000 kwacha mwa katundu wina yemwe wakwera kwambiri lero ndi ngozi yayikulu yomwe Malawi akugweramo yoti munthu opanda ukadaulo wa chuma sangakwanitse kukonza.
“Mbewu za Chimanga sizinasinthepo kuyambira 2017 pomwe ndinali gavanala, feteleza anali pa 18, 000 kwacha mpaka 2020, ndalama inali ya mphamvu, anayitenga ili pa 732 kwacha Ku dollah pano afika nayo pa 5,000 kwacha pa nsika wa nseli, ndithu akalowanso ayisuntha ifika 10,000 kwacha pa dollar imodzi awawa” anatelo a Kabambe.
Iwo anati akuwona sopo atafika pa 10,000 kwacha komanso, feteleza atha kufika 500,000 kwacha zomwe ziphe aMalawi mmagawo onse.
Mtsogoleriyu wati masankho a chaka chino akufunika alozele kukonza chuma chomwe chasakazika molapitsa.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi Mathews Mtumbuka anati boma la a Chakwera lakhala labodza kuyambira 2020 ndipo angobwera kudzasakaza zinthu ndikuzuza moyo wa aMalawi.
A Mtumbuka ati pogwiritsa ntchito ukadaulo omwe ali nawo akhale akusula achinyamata kukhala ndi luso ndi ukadaulo pa ma computer zomwe zidziwabweletsela ndalama malinga ndi momwe dziko likuyendera.
Gavanala wa chigawo cha pakati Rashid Phiri ati anthu apeza mavuto ochuluka chifukwa cha utsogoleri omwe uli pano, ndipo apempha anthu kusankha a Dalitso Kabambe kuti abwezeletse zinthu maka chuma mchimake.
A Kabambe ndi chipani chawo amachititsa misonkhano yoyima yima lero mu Madera a Matapira, Chowo ndi William Murray m’boma la Lilongwe pomwe akukonzekera kukapikisana nawo pa masankho a pa 16 September.