Wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Odya Zake Alibe Mlandu (OZAM) a Michael Usi ati akamakhala amadandaula kuti analoweranji m’boma.
A Usi ati zomwe awona iwo chiwasankhileni pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ndi zosasimbika.
A Usi amayankhula izi pa msonkhano oyimayima omwe anachititsa pa msika wa Wakawaka mu mzinda wa Lilongwe pamene anali pa ulendo opita mu mzinda wa Blantyre
A Usi omwe adasankhidwa kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino atamwalira a Saulos Chilima adzudzula utsogoleri wa a Lazarus Chakwera komanso chipani cha Malawi Congress kaamba ka mavuto adzaoneni omwe akuta dziko lino.
Mwachitsanzo, a Usi anatchulapo kukula kwa mchitidwe wa ziphuphu komanso katangale omwe akuti ukubwenzeletsa chitukuko m’dziko muno.
“Amene tawononga dziko lino ndi ife anthu omwe tili pa maudindo m’boma.Mwachitsanzo, anthu ena akamafuna kubweretsa chitukuko m’dziko muno timafuna kuti atinyemele Kaye kenakake zomwe zimapangitsa kuti ofuna kubweretsa chitukuku-wo anyanyale,” anatero a Usi.
A Usi atinso sanganenele bodza a Chakwera koma zomwe akunena ndi chilungamo chokhachokha.
Mtsogoleri wa Odya Zake Alibe Mlandu-yu wapempha anthu onse m’dziko muno kuti agwirane manja posatengera mitundu ndipo azasankhe atsogoleri mwanzeru pa chisankho cha pa 16 September chaka chino.