MEC yadula mutu ofuna utsogoleri wa dziko atatu


Mbewe

Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) latchetcha pa mndandanda atsogoleri atatu kuti sakapikisana nawonso pa chisankho chofuna kusankha m’tsogoleri wa dziko lino mwezi wa mawa.

Malingana ndi bungweli lero, opikisana khumi ndi asanu ndi awiri (17) ndi omwe awavomereza kuti akapikisana nawo kupatulako a Daniel Dube a chipani cha Nationalist Patriotic party (NPP), a David Mbewe a chipani cha Liberation For Economic Freedom Party (LEFP) ndi a Hardwick Kaliya oyima pawokha kamba kakuti onsewa palibe pa mndandandawu ngakhale anapereka zikalata zawo.

Malinga ndi wapampando wa bungweli a Annabel Mtalimanja, atawunika zikalata za atsogoleri owonetsa chidwi makumi awiri (20) omwe anapereka zikalata zawo, malinga ndi malamulo iwo avomereza opikisana khumi ndi asanu ndi awiri kamba kakuti akwanilitsa zonse zofunika pa zikalata zomwe adaperekazo.

A Mtalimanja ati bungweli lavomeleza a Joyce Banda, Thokozani Manyika Banda, Akwame Bandawe, Lazarus Chakwera, Kamuzu Chibambo, Adil James Chilungo, Cosmas Chipojola, Dalitso Kabambe, Peter Mutharika, Atupele Muluzi, Phunziro Mvula, Frank Mwenefumbo, Kondwani Nankhumwa, Jordan Sauti, Smart Swira, Millward Tobias ndi a Michael Usi.

Bungwe la MEC pomwe linkalandira zikalata sabata yatha zowonetsa chidwi chofuna kupikisana nawo pa mpandowu ndipo lidatsindika kuti akatha kulandira zikalatazi ndikuzukuta pa gawo loyamba, iwo akazukutanso gawo lachiwiri ndi cholinga choti zonse zofunikira zikwanilitsidwe. 

Bungweli lidabwenza a Kaliya ndi a Dube pa gawo loyamba lomwe kuti akakonze zikalata zawo.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading