Dzikoli likufunika katswiri pa chuma osati mapemphero kapena malangizo okhaokha – Kabambe
M’tsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) Dalitso Kabambe wati iye akufuna a Malawi asankhe katswiri pa chuma kuti umoyo wa anthu ambiri usinthe, pomwe wati dziko lino silikungofunika mapemphero a Lazarus Chakwera okha kapena ulangizi wa malamulo wa a Peter Mutharika monga aliyense pa ukadaulo wake.
Polankhula pa misonkhano yawo m’boma la Mchinji, a Kabambe ati chuma chikayenda bwino zambiri zimasinthanso ndipo odziwa kuyendetsa chuma ndi iwo okha basi pa opikisana onse 17.
M’mawu awo mtsogoleriyu wati, ukadaulo wawo unawonekera pomwe anakonza chuma cha dziko lino mzaka za 2017 kufika 2014, ndipo anayesetsa kukweza chuma kuti ngakhale ziwongola dzanja zikhale zochepa zonsenzo mu nzeru ndi ukadaulo wawo.
A Kabambe ati iwo amadziwa kuchita kawuniniwuni ndi kudziwa zofunika kukonza msanga, umboni uli pa momwe mitengo ya katundu inalili mu ulamuliro wa a Mutharika pomwe iwo anali Gavanala wa Reserve Bank ndipo Bank-yi inayamba kupanga phindu kufika mpaka 7 billion kwacha kuchokera kosapanga phindu mu chuma.
“Sindikupempha Voti yanu kuti ndidzakutayitseni nthawi, ngati mukudwala ndipo mukufuna kusanjikidwa manja pitani kwa a Chakwera akakupempheleleni, ngatinso uzimuwo ulimo, ngati muli ndi mavuto a milandu pitani kwa a Mutharika iwo aja ndi akatakwe koma ngati mavuto anu ali kusowa kwa ndalama zakunja, mukwera mitengo kwa katundu, kusowa kwa ntchito, njala, malonda osayenda komanso umphawi sankhani Kabambe mu zaka ziwiri tidzakonza chilichonse” anatelo a Kabambe.
“Ndi zotheka kukhala ndi dziko lokoma lonyadilitsa” anawonjezera a Kabambe
iwo atsindikanso kuti anayesetsa kulimbana ndi ndalama ya Malawi kuyikonza kuti ikhazikike komanso pomwe amkachoka pa udindowu wa gavanala mdziko ndipo ngakhale ndalama za kunja zinali zokwanila kugwiritsa ntchito kwa miyezi isanu ndi umodzi kuchoka pa ndalama zongokwanila masabata awiri okha.
Pomwe dziko likumka ku masankho a pa 16 September, akatswiri pa ndale ndi zochitika mdziko, akhala akufotokoza za kuthera kwa a Dalitso Kabambe powayelekeza ndi atsogoleri ena omwe akufunanso mpando wa mtsogoleri wa dziko pomwe ati mwa atsogoleri onse omwe akufotokoza za momwe adzachitile zinthu zomwe akufotokozazo ndi a Kabambe okha.









