Mikangano yolimbirana malo m’boma la Chikwawa yatha – Mafumu


Chikwawa Shire Transformation Project

Mafumu a boma la Chikwawa ayamikira bungwe la Shire Valley Transformation komanso unduna wa za malo kamba kothana ndi mikangano yolimbirana malo m’bomali yomwe yakhala ikusowetsa mtendere mafumu wa poyiweruza.

M’modzi mwa mafumu andodo m’bomali Senior Chief Kasisi alankhura izi Lachinayi m’dera lawo pomwe bungwe la Shire Valley Transformation komaso ena mwa akulu akulu aku unduna wa za malo amapereka ziphaso za umwini wa malo kwa ena mwa anthu a m’bomali pansi pa ntchito yolembetsa umwini wa malo yomwe inayambika chaka cha 2018.

Polankhula pa mwambo wopereka ziphatsozi, mfumu yayikulu Kasisi anati boma la Chikwawa ndi imodzi mwa maboma omwe mikangano ya malo yakhala ikusowetsa mtendere mabwalo awo.

Malingana ndi mfumuyi, izi tsopano zikhala mbiri yakale ponena kuti kuperekedwa kwa ziphatso za umwini wa malo palibe yemwe angadzakhale ndi mphamvu zofuna kulanda malo awina chifukwa cha dzina lomwe liri pa chiphasocho.

“Lero ndine okondwa kuti anthu a mdera langa alandira ziphatso zawo za umwini wa malo zomwe zindithandizira ntchito yanga yokhazikitsa bata ndi mtendere pa mikangano yolimbirana malo yochuluka yomwe yakhala ilipo mdera lino kuti lichepe,’’ anatero a Kasisi.

Pomaliza, mfumuyi unapempha anthu ake kuti asagulitse malo awo ponena kuti malo ndi chuma chawo chokhazikika.

Ndipo polankhulapo mkulu woona ntchito za bungwe la Shire Valley Transformation a Stanley Khaila anati ntchito yolembetsa malo ya umwini m’boma la Chikwawa inayamba kutsatira kuchuluka kwa mikangano yolimbirana malo pamene bungweli linkayamba kugwira ntchito zake bomali.

Iwo anati pakadali pano mugawo lawo loyamba la ntchito yolemba umwini wa malo, anthu oposera 3,000 ndiwo alembedwa mu kaundula wa umwini wa malo m’bomali m’madera asanu a mfumu yaimkulu Kasisi, Katunga, Maseya, Ndakwera komanso m’dera la mfumu  Lundu.

Malingana ndi a Khaila, ntchito yolemba umwini wa malo m’bomalu ikadapitilira pomwe ikuyembekezeka kulowa gawo lina lachiwiri la ntchitoyi.

Mau awo, m’modzi mwa makomishonala ku unduna wa za malo omwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambowo kuyimirira mlembi wamkulu wa za malo ku undunawo, a Robins Lukasi anati ndi cholinga cha boma kudzera ku unduna wawo kuti ayike mu kaundula wa malo oposera mahekitala 11,000 dziko lonse.

Malingana ndi a Lukasi, pakadalipano mahekitala okwana 200,000 ndiwo alembedwa kale maboma a Chikwawa ndi Nsanje pamene undunawu ukuyembekezeka kulemba mahekitala a malo okwanira 11,000 m’dziko lonse.

Bungwe la Shire Valley Transformation likugwira ntchito yomanga makanala opatutsira madzi pa ulimi wamthilira m’boma la Chikwawa.

Ntchitoyi inayamba m’chaka cha 2017 ndipo ikuyembekezeka kudzafika kumapeto m’chaka cha 2030 ndi thandizo la ndalama zochokera ku World Bank, African Development Bank, boma la Malawi mwa ena.

Wolemba: Macmillan Mozeyo

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading