Pamene maso ali ku Lilongwe kuti mtsogoleri wakale wa dziko lino a Arthur Peter Mutharika apereke kalata zake, anthu atangwa kuti aone kuti iye ayenda ndi ndani.
Mqlipoti amene Malawi24 tapeza akuonetsa kuti mtsogoleriyu wasankha munthu wa mayi kuti ayende naye pa masankhowa.
Pamene tinafunsa atsogoleri ena achipanichi za nkhaniyi, iwo anangoyankha modula kuti sanganene zambiri.
“Atha kutenga mzimayi ndithu, sikuti alipo adandaule,” mmodzi anatero kenako kudula foni titawayimbira.
