Ife koma a Mutharika atsogole ndi a Kabambe pambuyo – atero a Malawi mu kafukufuku
Akakhala a Mutharika apereka mapepala awo mawa lachisanuli. Ndipo a Malawi ambiri ali ndi chidwi, maso kunjira, kufuna kuona atenga ndani maka pano pamene zikuoneka ngati zokambirana ndi chipani cha UTM sizinasonye kwenikweni a Chihana ataulura kuti a Mutharika atenga wachiwiri wawo mu DPP momwe. Koma kutengera maganizo a anthu ochuluka, ati iwo bola a Mutharika a ku Thyolo atengane ndi a Kabambe a ku Thyolo. Iwo patsogolo, a Kabambe owathandizira.
Kafukufuku amene tsamba lino lachita waonetsa kuti a Malawi ochuluka afunitsitsa kuti a Peter Mutharika atengane ndi a Kabambe pa masankho amene akubwera mu mwezi wa Seputembala. Malinga ndi kafukufukuyi amene anali otsegulidwa pa tsamba lathu, a Malawi okwana 65 pa 100 alionse anavota kuti mgwirizano omwe akuona utachitira bwino voti yawo ndi wa awiriwa.
Kumapeto kwa sabata latha, Malawi24 idafunsa anthu kuti apereke maganizo awo pa mgwirizano wa zipani. A Malawi ambiri adanenetsa kuti iwo akufuna kuti zipani za DPP, UTM ndi AFORD zipange mgwirizano. Ambiri amafotokoza kuti iyi inali njira yokhayo yofuna kugwetsa MCP imene adayidandaula kuti ikudzetsa mavuto ochuluka.
Potsatira pamenepa, Malawi24 idafunsanso kuti anthu asankhe kayimidwe kamene akukaona kuti ndi ka phindu. Padali a Mutharika ngati otsogolera, kuti achiwiri awo akhale a Kabambe pamene pena panali a Kabambe ngati otsogolera, kuti wachiwiri wawo akhale a Mutharika, kapena mwina a Mutharika ngati ostogolera ndi kuti wachiwiri wawo akhale a Chihana a AFORD. Pamapeto panali a Kabambe ngati otsogolera kuti wachiwiri wawo akhale a Alfred Gangata.
Pamapeto pa masankho oyeselera amenewa, anthu pafupifupi 5100 adasankha kuti a Mutharika atsogore ndipo atenge a Kabambe ngati woyenda nawo. Anthu ena okwanira 2421 ndiwo adasankha kuti a Kabambe akhale otsogolera ndipo a Mutharika akhale owaperekeza. Izi anthu ena adatsutsa kuti sizingatheke potengera kuti a Mutharika ndi mtsogoleri wakale ndi munthu wachikulire ndiye sangamakakhale pansi pa a Kabambe.
Anthu ochepa chabe ndiwo adasankha kuti a Mutharika atenge a Chihana kapena kuti a Kabambe ayime ndi a Gangata. Anthu oganiza chonchi sanapitilire 300 ndi komwe.
Koma ngakhale a Malawi ochuluka aoneka ngati akanakondwa kuti a Mutharika atengane ndi a Kabambe, izi ndi zokayikitsa pamene chipani cha DPP ndi chipani cha AFORD zalengeza kuti zagwirizana. Iwo ati mwa zina a AFORD avomera kuti chipani cha DPP chizasankhe mtsogoleri oyenda ndi a Mutharika mu chipani chawo pa masankhowa. Iyi ndi mfundo imene yakhala ikuvuta anthu amene akufuna ubale ndi chipani cha DPP.
Malinga ndi ena, palibe ubale umene anthu ayembekezere kuwuona pakati pa DPP ndi UTM pa masankho akubwerawa. Zokhumba za anthu izi zikuoneka ngati zilephereka kukwaniritsidwa.
