A Malawi 31 amangidwa ku Tanzania ndi thambi yowona zolowa ndi zotuluka

Advertisement
Illegal Immigrants Tanzania

A Malawi okwana 31 ali m’gulu la anthu omwe amangidwa ndi nthambi yowona zolowa ndi kutuluka kwa anthu ya dziko la Tanzania.

Malinga ndi Mkulu wa nthambi ya Immigration mumzinda wa Dar es Salaam, Vincent Haule watsimikizira Malawi24 kuti a Malawiwa adamangidwa chifukwa choganiziridwa kuti akhala akukhala m’dzikolo mopanda zikalata zovomerezeka.

 “Ndizoona kuti tamanga a Malawi okwana 31 pamodzi ndi anthu ena ochokera m’mayiko ena. Anthuwa akhala akukhala m’dziko lathu lino mopanda zikalata zowayenereza, choncho tikuona kuti akuyika chitetezo cha dziko lathu pa chiwopsezo ndipo Rawatsegulira mlandu,” watero Haule.

Anthuwo anagwidwa pakati pa 19 ndi 22 July, 2025, pomwe nthambiyi inkachita chipikisheni cha nyumba pa nyumba.

A Malawi ena omwe Malawi24 tinakwanitsa kuyankhula nawo, ati nthawi yomwe anali kugwidwa, amawapeza atagona ndipo amawatenga usikuwo ndi kuwaika m’magalimoto.

Ku Malawi kuno kulinso anthu ambiri ochokera ku Tanzania omwe akuchita malonda osiyanasiyana kuyambira mzinda wa Mzuzu ku msika wa Mataifa ku Nkhata Bay ndi madera ena.

Malawi24 yapezanso kuti m’boma la Mzimba, mzika zina za ku Tanzania zakhala zikupanga renti m’nyumba za boma za Malawi House zomwe zili ku dera la staff.

Ofesi ya Kazembe ya Malawi ku Tanzania yati sikudziwapo kanthu za kumangidwa kwa a Malawi ochuluka chonchi.

Advertisement