Pomwe akulu akale adati ukanama sikuchedwa kucha, mwambiwu ku nyumba ya chifumu sukuwatekesa. Chitadzodza matope achinyamata pa nkhani yowathetsera ulova, chipani cha MCP motsogozedwa ndi mtsogoleri wake Lazarus Chakwera chati chikangowina chisankho ulendo uno, ulova mdziko muno ikhala nkhani ya make dzana.
Ngakhale kuti chipani cha MCP chalephera lonjezo lake lothandiza achinyamata 1 miliyoni kupeza ntchito, ulendo uno chipanichi chati chipezera ntchito achinyamata okwana 3 miliyoni, zomwe ambiri akutsutsa ponena kuti ndi maloto achumba chabe, ndipo ambiri akufusana, “Kapena ntchito yake ndi yonyamula zikwanje kukhapa aziwonetsero?”
Malingana ndi mfundo zokopera anthu zomwe MCP yakhazikitsa Loweluka, ikangopambana chisankho pa 16 September pano, anthu 1 miliyoni apeza ntchito zokhudza ulimi, 500,000 ntchito zokhudza kupanga zinthu m’mafakitale, komanso 500 ena ntchito za zomangamanga.
Kuwonjezera apo, chipanichi chati anthu enaso 1 miliyoni adzalembedwa ntchito m’nthambi zosiyanasiyana kuphatikizapo za chitetezo, zokopa alendo, komanso ku nthambi ya za migodi.
Potengera momwe boma la MCP lagwilira ntchito m’zaka zisanu zapitazi, anthu ambiri m’dziko muno ati mfundo za chipanichi ndi bodza landiwolotse. Ambiri ati ndikovuta kulemba anthu 3 miliyoni ntchito pomwe zidavuta kale kulemba anthu 1 miliyoni.
“Koma zinazi ndizongofuna kutapana mkamwa ndithu, ngati mwakanika ntchito 1 million, nde 3 million mukwanitsa, aaa musatiyese, uku nkungofuna mavoti basi musatinyasepo apapa,” watelo Thomas Twea poyikira ndemanga za nkhaniyi pa tsamba lina pa fesibuku.
Koma ngakhale anthu akuiloza chala MCP kuti yalephera kulemba anthu ntchito 1 miliyoni, mu mfundo zake zokopera anthu chipanichi chati pa zaka zisanu zapitazi chalemba anthu ntchito 2,408,634 zomwe ati zikuwapatsa mangolomera kuti kulemba anthu ntchito 3 miliyoni ikhala ntchito yophweka.









