Anthu asauka kwambiri zaka zisanu za MCP – Phiri


Anthu asauka kwambiri zaka zisanu za MCP - Phiri- Malawi24

Yemwe akufuna kudzayimira ngati phungu wa nyumba ya malamulo ku dera la kumpoto chakumvuma kwa boma la Dowa, Pemphero Phiri wati anthu ku derali akonzeka kudzasankha chipani cha United Transformation kamba kazokhoma zomwe awona mu ulamuliro wa Malawi Congress Party (MCP).

Poyankhula ndi Malawi24, Phiri anatchula njala komaso umphawi ngati zinthu zomwe zasautsa kwambiri anthu ku delali.

“Anthu ndiwokhumudwa chifukwa pa zaka zisanu zomwe MCP yakhala ikulamula, anthu akudela kwathu akhala akuvutika kugula feteleza weniweniyu ngakhale delali limadalira ulimi moti tikukamba pano anthu ena omwe analembedwa chaka chatha koma mpaka pano sanagulebe feteleza chifukwa sanabwere”

“Mavuto ndie ndiwosanena, anthu asauka zaka zisanuzi ngakhale ali olimbika kugwira ntchito” anatero Phiri.

Phiri anatuluka MCP miyezi iwiri yapitayi kutsatilaso kulephera kupikisana nawo pazisankho zachipulura mchipanichi pomwe ananyanyala ponena kuti panali zolakwika zambiri. 

Iye wati ndiwokondwa kuti UTM inamulandira bwino ndipo mfundo zachipanichi zili ndikuthekera kosintha dziko la Malawi.

Malingana ndi Phiri, chilowele mchipani cha UTM wakhala akuwauza anthu ku dela lake za ukadaulo pa zachuma wa mtsogoleri wachipanichi Dalitso Kabambe zomwe zakopa anthuwa kuti atsimikize zodzayika UTM m’boma.

Kumbali yake, Phiri wati akuyembekezeka kutsekulira ulimi wa mthilira, ulimi wa njuchi komaso kupeleka ngongole kwa anthu ndicholinga chofuna kutukula miyoyo yawo kuti adzitha kudziyimila pawokha pa chuma komaso chakudya.

Phiri anasiya ntchito kunthambi yazofalitsa ma uthenga ku nyumba ya boma pofuna kukwanilitsa khumbo lake lodzakhala phungu wa nyumba yamalamulo.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading