Mfumu yayikulu Kumtaja yayipidwa posapatsidwa mpata olankhula pamaso pa a Chakwera


Mfumu yayikulu Kumtaja yayipidwa posapatsidwa mpata olankhula pamaso pa a Chakwera- Malawi24

“Ndakwiya kwambiri” yatelo mfumu yayikulu Kumtaja ya m’boma la Blantyre ponena kuti ndi yokhumudwa kwambiri posapatsidwa mpata kuti ilankhure pomwe mafumu a m’bomali amakakumana ndi kucheza ndi m’tsogoleri wa dziko Lazarus Chakwera ku nyumba ya boma ya Sanjika mu mzinda wa Blantyre.

Mfumuyi yati mafumu amakakumana ndi a Chakwera lachitatu lathali, ndipo ati iwo monga mwini dera sadapatsidwe mpata olankhura pamaso pa mtsogoleri wa dziko ndipo m’malo mwake analankhulira mafumu onse a m’boma la Blantyre anali mfumu yayikulu Kunthembwe. 

Malinga ndi ma ripoti, mfumuyi ati inalawilira kukapereka dando lakeri ku nyumba yofalitsa nkhani ya Zodiak komwe inakati iyo ndi yosakondwa ndi yoyipidwa, poti ndi yomwe imayenera kulankhula chifukwa nyumba ya chifumu ya Sanjika ili mu dela lake.

“Apulezidentitu akudziwa kuti dera lija ndi langa, a director of chiefs a Makanga ndi a DC alipowa akudziwa kuti ndi dera langa, ndiye ife tikudabwa kukatenga gogo chalo wa dera lina kulankhula pamaso pa pulezidenti, ndakwiya kwambiri” mfumuyi inawuza wayilesiyi.

Izi anthu ena poyikira ndemanga ati mfumuyi simayenera kudzikundikira chifukwa nyumba ya chifumu ndi ya mu dera lawo ndipo amangoyenera amvetsetse.

Pomwe ena mu ndemanga zawo ati kusemphanitsa olankhulaku kunawonetsa kuchepsya Mfumuu Kumtaja.

Mtsogoleri wa dziko linoyu ali ku chigawo cha kummwera komwe akucheza ndi adindo osiyana siyana monga mafumu, atsogoleri a mipingo ndi ena.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading