Phungu wa nyumba yamalamulo wa dera lapakati pa boma la Mangochi, Victoria Kingstone watuluka chipani cha Democratic Progressive (DPP) pomwe tsopano adzayime payekha pazisankho zapa 16 September.
Polengeza kutuluka kwake muchipani cha DPP, Kingstone wati adzigwiritsabe ntchito makaka obiliwira ngati a DPP komano pazovala za otsatila ake chasintha ndi chizindikiro chomwe tsopano chikhale ndi nkhokwe yachimanga yodzadza kusiyana ndi DPP yomwe pali chimanga chinayi.
Malingana ndi Kingstone, kusintha chizindikiroku kwabwera chifukwa chimanga chinayi sichokwanira kudyetsa anthu ochuluka.
“Kodi chimanga chinayi ndi chimanga chodzadza nkhokwe chimadyetsa mudzi ndichiti? Ine ndipitiliza ndimakaka obiliwira koma chizindikiro ndasintha kuyika chimanga chodzadza nkhokwe,” anatero Kingstone.
Kutuluka mu DPP kwa Kingstone kunadza kamba kakusamvana komwe kunalipo ku delari pa zisankho zachipulura zomwe a Kingstone anadandaula kuti panali zolakwika zambiri.
Ngakhale Kingstone anadandaula, koma DPP inapitilira ndiganizo lake lochititsabe chisankhochi.
Rota Fatch Mbilizi anapambana kudelari ngati woyimila DPP ndipo anadutsa opanda opikisana naye, kutsatilanso kusatenga nawo gawo pazisankhozi kwa Victoria Kingstone.
