Chipani cha Malawi Congress chati ndichokonzeka kuyamba misonkhano yokopa anthu pokonzekera masankho a patatu omwe adzachitike m’dziko muno pa 16 Sepitembala.
Izi zikudza pomwe bungwe loyang’anira chisankho la MEC likhale likukhazikitsa tsiku loyamba kupangitsa misonkhanoyi sabata yamawa.
Phungu wa nyumba ya malamuro wa m’dela la kumpoto kwa boma la Chikwawa a Owen Chomanika ndiye walankhula izi Lolemba pomwe amakumana ndi makomiti ake achipani pokonzekara chisankho chikudzachi.
Chomanika, yemwenso ndi nduna yoona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo wati iye ndi chipani chake akonzeka kupanga ndale zodzapambana pa chisankhocho.
Malingana ndi phunguyu, boma la a Lazarus Chakwera lakwanitsa kutumikira anthu moyenerera kotero ndikofunika kuti apitirize kutumikira anthu m’dziko muno powapatsanso zaka zina zisanu.
“Sindinakwanitse m’magawo ena aza chitukuko komabe ndayesesa kwambiri. Ndikuyimaso kuti ndipitirize kukutumikirani m’magawo ena otsalawo ndi cholinga choti umoyo wanu mdera lino usinthike koposa,” Chomanika analankhula motero.
Pamwambowu, Chomanika anagawanso thandinzo la ufa kwa anthu ake ponena kuti iye akudziwa bwino lomwe za njala yomwe yakhudza dela lake komanso dziko.
Iye anatsimikizira anthuwo kuti apitiriza kupereka thandizo la chakudya magawo onse a m’dela lake kuti uluru wa njala uchepeko.
Koma polankhulapo, m’modzi mwa atsogoleri akomiti ya chipani m’delalo a Grace Kaliati anati iye ngati m’dindo alimbikitsa bata ndi mtendere pa nthawi yomwe zipani zizichititsa misonkhano ponena kuti zipolowe zitha kupangitsa kutaya anthu omwe ali ndikuthekera kudzasintha chuma cha dziko lino kudzera pakutenga kwawo pagawo loponya voti lawo posankha atsogoleri aluntha pa utsogoleri popereka chitsanzo cha phungu wawo Chomanika komanso mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera.
Iye wathokonzaso phungu wake pathandizo la chakudya ponena kuti phunguyu waonetsa mtima okonda anthu ake ndi mtima wake onse ndipo ali pambuyo pake komanso a Chakwera pa chisankkho chikudzachi.
Bungwe la MEC lolemba pa 14 Julaye sabata la mawa likuyembekezeka kutsegulira ntchito yokopa anthu pa chisankho chikudzachi.
Ntchito yokopa anthu ikuyembekezeka kufika kumapeto m’sabata yoyamba ya mwezi wa Sepitembala pomwe chisankho chomwe chidzachitike pa 16 mwezi omwewo chosankha mtsogoleri wa dziko, Phungu wa kunyumba ya malamuro komanso khasala.
Zisankhozi zimachitika pakamodzi pakatha zaka zisanu zilizonse kutsatira lamuro yomwe dziko lino linakhazikitsa kuti adindo onsewa adzikhala pa mipandoyi pakamatha zaka zisanu kuti aperekenso mwayi kwa anthu omwe awatumikira kuti asankhenso atsogoleri ena kapena kuwasankhanso ngati akhutitsidwa ndi ntchito zawo pa zaka zisanu zapitazo.
Wolemba: Macmillan Mozeyo
